23/08/2025
" dinari!!!" dinariiii"
_____________________________________________
Lero tiyeni tilowe nawo mu dziko ili la KUWAIT. Dziko la Kuwait lili ku Middle East
ndipo limalumikizana ndi maiko ena aakulu monga IRAQ ku kumpoto ndi SAUDI ARABIA ku kumwera. Mbali ina, lilinso ndi nyanja yotchedwa PERSIAN GULF, yomwe amagwiritsa ntchito posenza mafuta kupita ku maiko ena.
Dziko la Kuwait ndi laling'ono, koma ndi limodzi mwa maiko olemera kwambiri padziko lapansi. Izi zili tere chifukwa dzikoli limapeza ndalama zambiri kuchokera ku mafuta achilengedwe. Mafutawa amagwiritsidwa ntchito kupanga petulo, dizilo, ndi zinthu zina zomwe maiko ambiri amafuna.
Ndalama ya ku Kuwait imatchedwa KUIWAITI DINAR, ndipo ndi yamphamvu zedi. Kuwaiti Dinar imodzi ili ofanana ndi pafupifupi 5,700 Malawi Kwacha. Ndipo chifukwa cha kusiyana kumeneku, anthu ambiri amafuna kukagwira ntchito ku Kuwait kuti apeze ndalama zambiri.
Anthu ambiri a ku Kuwait amapeza ndalama mwa kugwira ntchito m'makampani opanga mafuta. Ndalama zimene dzikoli limapeza, limagwiritsa ntchito kumanga misewu wabwino, zipatala, mashopu akulu, komanso nyumba zazitali za m’tauni.
Pena mabwana amatuma antchito awo kuti alengezetse mmizinda zoti kukufunika antchito, ndiyeetu kumakhala kufuula ndi ma sipika , kukuwa ndithu kuti '" DINARIIII, DINARII" apopo amene ndi lova amayenera kusunzira kufupi ndi kumene kukumveka uthengako, ntchito sisowa kwenikweni.
Anthu ambiri ochokera ku Malawi ndi mayiko ena amapita ku Kuwait kukagwira ntchito monga ya mnyumba, ogwira ntchito yoyeretsa, ogwira ntchito yomanga nyumba, ulonda komanso m'ma hotelo. Ngakhale ntchitozi sizapamwamba ku Kuwait, amalipidwa bwino poyerekezera ndi ntchito zina zaku Malawi, ndipo zimawathandiza.
Ndalama ya ku Kuwait imatchedwa KUIWAITI DINAR, ndipo ndi yamphamvu zedi. Kuwaiti Dinar imodzi ili ofanana ndi pafupifupi 5,700 Malawi Kwacha.
Anthu ambiri a ku Kuwait amapeza ndalama mwa kugwira ntchito m'makampani opanga mafuta. Ndalama zimene dzikoli limapeza, limagwiritsa ntchito kumanga misewu wabwino, zipatala, mashopu akulu, komanso nyumba zazitali za m’tauni.
Pena mabwana amatuma antchito awo kuti alengezetse mmizinda zoti kukufunika antchito, ndiyeetu kumakhala kufuula ndi ma sipika , kukuwa ndithu kuti '" DINARIIII, DINARII" apopo amene ndi lova amayenera kusunzira kufupi ndi kumene kukumveka uthengako, ntchito sisowa kwenikweni.
Anthu ambiri ochokera ku Malawi ndi mayiko ena amapita ku Kuwait kukagwira ntchito monga ya mnyumba, ogwira ntchito yoyeretsa, ogwira ntchito yomanga nyumba, ulonda komanso m'ma hotelo. Ngakhale ntchitozi sizapamwamba ku Kuwait, amalipidwa bwino poyerekezera ndi ntchito zina zaku Malawi, ndipo zimawathandiza.
Chiarabu ndi chilankhulo chawo chomwe ndichofala, koma chingelezi chimagwiritsidwa ntchito kwambiri m'maofesi, mashopu, ndi zipatala.
Likulu la dziko la Kuwait limatchedwa Kuwait City. Mu city iyi muli muli matawa, nyumba zazitali, komanso malo ambiri owonera zinthu, mashopu akuluakulu, ndi malo achikhalidwe.
BWANJI TIFIKE MU MADERA ENA A MDZIKO ILI KUTI TIONEKO ZINA NDI ZINA?
PANGANI LIKE PAGE ILI LA Mfumu Solomo - Pabwalo TIYENDERE LIMODZI PA ULENDOWU