21/07/2025
wa chisankho #
M'tsogoleri wa chipani cha UTM a Dr Dalitso Kabambe wati nkhani ya njala, kusowa kwa ntchito pakati pa achinyamata, mavuto a zachuma ndinso kukwera mtengo kwa katundu udzakhala mbiri chabe chipani chake chikalowa m'boma chaka chino.
M'tsogoleriyu wanena izi lolemba la pa 21July m'boma la Dedza pa msonkhano wokopa anthu omwe umachitikira pa bwalo la sukulu ya Umbwi m'bomalo.
A Kabambe ati mavuto osiyanasiyana omwe dziko lino likukomana nawowa adzakhala nthano anthu akadzamuvotera kukhala mtsogoleri wa dziko lino pa chisankho cha pa 16 September.
"Mukuyenera kuponya voti yanu mwanzeru ngati mwatopa ndi mavuto omwe tikukomana nawo mdziko muno posankha chipani cha UTM chomwe chithandize kusintha zinthu mdziko muno kuti ziyambe kuyendaso ngati kale" iwo anatero.
Annie Phiri
PBWtv Lilongwe.
21/07/2025.