25/01/2023
BWATO LIGUBUDUZIKA KU MPOTO KWA BOMA LA NSANJE.
Ma lipoti amene akuchokera ku mpoto kwa Boma la Nsanje atsimikiza kuti Bwato lagubuduzika ndipo anthu ambiri akhudzika ndi ngoziyi.
Chimene chinachitika mchakuti alimi anatengana mwa nthawi zonse ndi ma banja awo kuwoloka doko kupita kwa Jambawe ku ma minda awo ndipo atafika pa dera lotchedwa Chuluchamkango ma Bwato awo anagubuduzika.
Chitsimikizo kuchokera ku Nsanje Trinity Hospital, zikusonyeza mwana m'modzi wamwalira ndipo anthu ambiri Ali mchipatalachi kulandira thandizo pa makina opereka mpweya (Oxygen) kotero kuti chiwerengerochi chitha kuchuluka.
Pamene timalemba mkuti mabwato onse asakuyenda pamalopa kuthandizira kuyang'ana anthu ena amene sadapezekebe. Kunali Mfuwu ochuluka pamalopa
Polankhula ndi Mphungu wa Nyumba ya malamulo kuyimirira ku mpoto ku Nsanje, Hon Enock Chizuzu. Iwo anati Ali okhudzika zedi ndi Ngoziyi, ndipo achita chothekera kuthandiza ma banja ovulalawa.
"Ndakhala ndikulangiza oyendetsa ma bwato kuyenda mosamalitsa nthawi ngati ino pamene kwathu kuno kumavuta madzi. Komanso oyendetsa ma bwato timawapempha asamanyamule katundu komanso anthu ochuluka mu bwato limodzi." Chizuzu kulankhula mokhudzika
Zambiri tikupatsirani pa
Ma lipoti amene akuchokera ku mpoto kwa Boma la Nsanje atsimikiza kuti Bwato lagubuduzika ndipo anthu ambiri akhudzika ndi ngoziyi. Chimene chinachitika mchakuti alimi anatengana mwa nthawi zonse ndi ma…