ITM Online TV

ITM Online TV News, Live coverage and livestreaming of various government, corporate and community events

02/06/2025

Malawi gears up for food systems transformation implementation with NPC's Research Manager, Dr. Andrew Jamali optimistic that the program will turn around the country's nutrition situation.

GIZ has also committed to supporting the implementation of the program to ensure that it achieves it's intended goals.

More in the interviews below:

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera wati achinyamata akuyenera kumapatsidwa mwayi okumana naye ndikupereka ma...
21/02/2025

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera wati achinyamata akuyenera kumapatsidwa mwayi okumana naye ndikupereka maganizo awo pa momwe akufunira kuti ntchito za chitukuko zidziyendera.

A Chakwera amalankhula izi pamwambo omwe achinyamata amawafunsa mafuso mu mzinda wa Lilongwe ngati njira imodzi yowadaiwitsa zomwe boma likuchita komanso kunva nkhawa za achinyamatawa.

Mwambo ngati omwewu ukachitikanso mu mzinda wa Blantyre pa 27 February komanso ku Mzuzu pa 4 March chaka chino.

20/01/2025

A Fatuma Mateyu omwe amachokera m'boma la Mangochi alandila mphoto yawo ya galimoto ya mtundu wa Mitsubishi Expander yomwe ndiya ndalama zoposa K60 miliyoni.

Polankhula atalandila mphotoyi, a Fatuma Mateyu ati ndiothokoza kwambiri ku kampani ya Mukuru ndipo akupempha a Malawi ambiri kuti alembetse pa Mukuru wallet kuti nawonso adzapeze nawo mphoto.

A Fatuma Mateyu akufotokoza zambiri:

17/01/2025

Kampani yotumiza ndi kulandira ndalama ya Mukuru, yati ndiyokondwa ndi momwe anthu akulandilira ntchito zake m'dziko muno.

Mkulu wa kampaniyi ku Malawi kuno a Pride Sam Chiwaya, ndi omwe amalankhula izi pamwambo osankha yemwe wawina mphoto yaikulu yomwe ndi ya galimoto la mtundu wa Mitsubishi Expander yomwe ndi ya ndalama zokwana K60 miliyoni.

Pa mayelewa, anthu ena awina mphoto monga kanema, foni, ma T-shirt komanso zipewa. Mu mpikisanowu, mumalowa anthu okwana 4305.

A Pride Chiwaya akufotokozapo zambiri:

17/01/2025

Fatuma Mateyu from Mangochi wins the ultimate prize of car Mitsubishi Expander worth MWK 60 million in the Kuiphula ndi Mukuru. The draw was conducted at Mukuru Head Office in Lilongwe.

This is how it was when officials from Mukuru called her to break the news .

21/12/2024

Atolankhani olemba nkhani zamasewero a mpira ku nyumba zowulutsira mawu komanso za kanema zosiyanasiyana, awapempha kuti adzilemba nkhani zawo potsatsa malamulo ndi ukadaulo wabwino pa nkhani zamasewerawa.

Mtsogoleri wa bungwe loona za masewera a mpira m'dziko muno la FAM, a Fleetwood Haiya ndi omwe amalankhula izi mu mzinda wa Lilongwe potsekera maphunziro a atolankhani pa zakalembedwe kwabwino pa nkhani zokhudza mpira.

M'mawu ake, wapampando wa komiti yoona za atolankhani ku bungwe la FAM, a Gray Phiri, ati maphunzirowa abwera pa nthawi yabwino ndipo akukhulupilira kuti aona kusintha pa kalembedwe kabwino ka nkhani zokhudza masewera a mpira.

A Grey Phiri akufotokoza zambiri:

17/12/2024

Bungwe lopititsa patsogolo maphunziro a atsikana m'dziko muno la CAMFED Malawi lati lipitilira kugwira ntchito zake mpaka litathandiza atsikana oposera 800,000 pofika mchaka cha 2030.

Polankhula pomwe amasainirana mgwirizano opereka thandizo latsopano pamaphunziro a atsikana ndi unduna wa za maphunziro m'dziko muno, mkulu wa bungwe la CAMFED Malawi a Susan Silika ati nzochititsa chidwi kuti pakadali pano, miyoyo ya atsikana omwe athandizidwa ndi bungwe lawo yasintha.

A Silika akufotokoza zambiri:

President Lazarus Chakwera arrives in the country from UAE , optimistic that Malawi will soon be experiencing fuel suppl...
10/12/2024

President Lazarus Chakwera arrives in the country from UAE , optimistic that Malawi will soon be experiencing fuel supply stability and foreign investment.

10/12/2024

Phungu wa dera la Machinga North East a Ajilu Kalitendele kulankhulapo pa mphekesera zomwe zikumveka kuti zisankho za aphungu anyumba ya malamulo ku dera kwawo sizinayende bwino.

A Kalitendele akufotokozapo zambiri:

10/12/2024

Mtsogoleri otsutsa boma ku nyumba ya malamulo a George Chaponda apempha boma kuti likuyenera kuonetsa kuti ma ufulu a aMalawi akulemekezedwa.

A Chaponda amalankhula izi pomwe amaonetsa kudandaula kwawo pakuchuluka kwa nkhani zopondeleza ufulu wa anthu omwe akufuna kuchita zionetsero za bata m'dziko muno.

A George Chaponda akufotokoza zambiri:

09/12/2024

Membala wa komiti yoona za chuma ku nyumba ya malamulo a Mary Navicha ati boma likuyenera kukhala losamala pa kayendetsedwe kake ka chuma.

A Navicha amayankhulapo mu nyumbayi pomwe amayankhapo paza lipoti la zachuma lomwe laperekedwa mu nyumba ya malamulo ndi nduna yoona za chuma.

Mwazina, a Navicha ati nzonvetsa chisoni kuti boma labweretsa lachulutsa kupempha ndipo nawonso opereka thandizolo sakukwanitsa lonjezo lawo.

A Mary Navicha akufotokoza zambiri:

09/12/2024

Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu apempha nyumba zofalitsa nkhani kuti zikhale zikulemba nkhani zoona zokhazokha pomwe tikuyandikira nthawi ya chisankho.

A Kunkuyu amalankhula izi pomwe amatsegulira msonkhano wapachaka wa anthu komanso nyumba zofalitsira nkhani.

M'mawu ake, mkulu wa bungwe la MACRA, a Daud Suleman ati nyumba zofalitsa nkhani zipewe kufalitsa nkhani zodzetsa chisokonezo powulutsa nkhani zokhazo zomwe afufuza bwino komanso anva mbali zonse.

A Kunkuyu ndi a Suleman akufotokoza zambiri:

Address

Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when ITM Online TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to ITM Online TV:

Share