We Can Media Online

We Can Media Online "The Voice of The Voiceless"

 Malawi's Scorchers have made history by reaching the quarter-finals of the 2026 Women's Africa Cup of Nations (WAFCON) ...
06/08/2026



Malawi's Scorchers have made history by reaching the quarter-finals of the 2026 Women's Africa Cup of Nations (WAFCON) on their tournament debut after finishing top of Group C, despite a 2-1 defeat to Zambia on August 5 in Morocco.

Coach Lovemore Fazili's side finished level on six points with Zambia and Nigeria in a tightly contested Group C. Malawi secured top spot after the Confederation of African Football (CAF) applied the tournament's tie-break rules following the final round of matches.

Although the Scorchers lost to the Copper Queens in Rabat, the result was not enough to deny them first place, capping off a dramatic and impressive group-stage campaign.

It is the first time the Scorchers have progressed beyond the group stage at WAFCON, marking a historic milestone for women's football in Malawi.

Reported by Noel Mtanga-Lilongwe(6/8/2026)

  newsBungwe la olemba nkhani zokhudza kusitha kwa nyengo la Network of Climate Journalists ( NCJ) lapempha boma komanso...
06/08/2026

news
Bungwe la olemba nkhani zokhudza kusitha kwa nyengo la Network of Climate Journalists ( NCJ) lapempha boma komanso mabungwe omwe siya boma omwe amagwira ntchito zokhudza za nyengo ndi kusitha kwa nyengo kuti agwiritse ntchito olemba nkhani ovomelezeka pa nkhani yokhudza nyengo ya EI Nino.

M'mawu ake wapampando wa bungweli Dietrich Frederich wati anthu ambiri akugwiritsa ntchito masamba amchezo pofakitsa nkhani zabodza zokhudza nyengo ya EI Nino momwe ikhudzire dziko lino zomwe ATI zokusoneza alimi mdziko muno.

" Dziko lino lili nawo olemba nkhani omwe amadziwa bwino kulemba nkhani nyengo komanso kusitha kwa nyengo, choncho boma komanso mabungwe omwe siya boma akuyenera kugwiritsa ntchito anthu amenewa kuti afalitse uthenga oyenelera ku mtundu wa a Malawi kuti alimi anthu adziwe chowona chenicheni zokhudza El Nino komanso mavuto omwe angabwere" Frederich anafotokoza.

A Frederich wapempaso mabungwe akufuna kwabwino kuti athandizire bungwe la NCJ ndi maphunziro ofuna kukumbutsira olemba nkhani m'mene angagwilire ntchito yawo.

Iwo ati alimi akuyenera kutsatira ma uthenga ochokera kwa olemba nkhani komanso nyumba zofalitsa nkhani zovomelezeka ponena kuti ma uthengawo amakhala ovomelezeka ndi boma komanso nthawi yowona za nyengo ndi kusitha kwa nyengo.

Wolemba: Emma Ngwata

 # WCM News Timu ya Chimbiya Stars yabwera pamwamba pa mpikisanowu wa Gojet Investments Division one itagonjetsa timu ya...
05/08/2026

# WCM News

Timu ya Chimbiya Stars yabwera pamwamba pa mpikisanowu wa Gojet Investments Division one itagonjetsa timu ya Airborne Rangers ndi zigoli ziwiri kwa duu masewero omwe anali pa bwalo la zamasewero la Linthipe Secondary school Ground m'boma la Dedza.

Zigoli za Crifton Lomos komanso Ishmael Saidi zomwe zathandizira timuyi kubwera pamwamba pa mpikisanowu.

M'mawu ake mphunzitsi wa timuyi Paul Pogba wati chipambanochi chadza kamba kakuchilimika kwa anyamata ake choncho wati iye ndiwokondwa ndi zotsatirazi.

Mphunzitsi wa timu ya Airborne Rangers Asedi Ayami wati kubwera kwa zigoli mwachangu ndikomwe kunasoneza osewera ake komanso kafikedwe kawo kanali kochedwaramo zomwe wati zathandizira timu yake kugonja masewerowa.

Pakadali pano timu ya Chimbiya Stars yasewera masewero okwana asanu ndi amodzi (6) yapambana anayi kufananitsa mphavu awiri ndipo ili ndi mapointi okwana 14.

Crifton Lomos ndi yemwe anasakhidwa kukhala osewera amene wasewera bwino kuposa azake m'masewerowa.

Wolemba: Emma Ngwata

Mtsogoleri wa dziko lino Proffesor Arthur Peter Mutharika akuyembekeza kuchoka mdziko muno kupita mdziko la South Africa...
05/08/2026

Mtsogoleri wa dziko lino Proffesor Arthur Peter Mutharika akuyembekeza kuchoka mdziko muno kupita mdziko la South Africa pa ulendo omwe si wa boma.

Ndege yonyamula a Mutharika ikuyembekezeka kuchoka kuno kumudzi kudzera ku bwalo la ndege la Kamuzu International Airport.

  Masters FC goalkeeper Brighton Munthali has officially left the club after completing his transfer to Tanzanian side M...
04/08/2026



Masters FC goalkeeper Brighton Munthali has officially left the club after completing his transfer to Tanzanian side Mbeya City FC.

Munthali held his final training session with Masters FC on Monday before saying farewell to teammates, coaches and officials.

Speaking after the session, Munthali thanked the club for its support. “I’m grateful to the management, coaches, my teammates and supporters. It was a privilege to wear this jersey and I wish the team success,” he said.

Chief Executive Officer Kelvin Moyo praised Munthali’s conduct. “Brighton has been a true professional and ambassador for Masters FC. We thank him and wish him well in Tanzania.”

Munthali made 6 FDH Premiership appearances this season, keeping 2 clean sheets and winning 1 Player of the Match award.

Reported by Noel Mtanga-Lilongwe(4/8/2026).

  Oyendetsa njinga zamoto zonyamula anthu, zomwe zimadziwika kuti kabaza, ku Lilongwe akukhala ndi mantha chifukwa cha m...
04/08/2026



Oyendetsa njinga zamoto zonyamula anthu, zomwe zimadziwika kuti kabaza, ku Lilongwe akukhala ndi mantha chifukwa cha machitidwe waza uchifwamba ndi chiwawa omwe wakhala ukuchitikira m'madera osiyanasiyana a mzindawu.

Poyankhula ndi tsamba lino, ena mwa oyendetsa kabaza ati nthawi zambiri amakumana ndi anthu omwe amawoneka ngati makasitomala koma kenako amawazunza kapena kuwabera ndalama ndi njinga zawo, makamaka usiku.

Mmodzi mwa oyendetsa njinga Aubrey Kumthembwe wapempha chitetezo kuti chiwonjezekele chifukwa ntchito yakabaza ndi yomwe imawasamalira, koma tsopano akugwira ntchitoyi ndi mantha.

Polankhapo pa nkhaniyi, polisi ya Lilongwe yati ikupitiriza kufufuza milandu yonse yokhudzana ndi chiwawa komanso kuba komwe kukukhudza oyendetsa kabaza. Iwo alimbikitsanso oyendetsa kabazawa kuti azitsatira njira zachitetezo monga kupewa kunyamula makasitomala kumadera amdima kapena osadziwika bwino usiku komanso kufotokozera mwamsanga zochitika zilizonse zokayikitsa.

A Foster Mwasiyano okhala ku dela la 38 ati chitetezo cha oyendetsa kabaza ndi chofunika chifukwa ntchito yawo imathandiza anthu ambiri kufika kumalo awo tsiku ndi tsiku komaso mwa nsanga.

Anthu akuyembekezera kuti mgwirizano pakati pa apolisi, oyendetsa kabaza ndi anthu ammudzi uthandiza kuchepetsa uchifwamba komanso kubwezeretsa bata mumzinda wa Lilongwe.

Wolemba Zakeyu Mamba -Lilongwe:4/7/2026

Bungwe la CDEDI lati likukhulupilira kuti ndondomeko zoyenera zitsatidwa mwansanga kuti mtsogoleri wake Slyvester Namiwa...
03/08/2026

Bungwe la CDEDI lati likukhulupilira kuti ndondomeko zoyenera zitsatidwa mwansanga kuti mtsogoleri wake Slyvester Namiwa atuluke mchitokosi.

Mneneri wa CDEDI Promise Thom wati apolisi asunga a Namiwa kwa masiku 4 popanda mlandu uliwonse ndipo lero akuyenera kudziwa chomwe analakwa.

Thom wati owayimira pa mlandu a Namiwa ali tcheru kuti atsate njira zoyenera komanso kupempha kuti atuluke pa belo.

Iwo atsindika kuti CDEDI siphethira ndipo lipitiriza kuunikira momwe adindo akugwirira ntchito yawo mdziko muno.

Thom wati iwo ndi othokoza kwa magulu onse omwe ayima nawo pa nthawiyi.

Wolemba: Jane Chirwa -Lilongwe

 Bungwe la CDEDI lati likukhulupilira kuti ndondomeko zoyenera zitsatidwa mwansanga kuti mtsogoleri wake Slyvester Namiw...
03/08/2026



Bungwe la CDEDI lati likukhulupilira kuti ndondomeko zoyenera zitsatidwa mwansanga kuti mtsogoleri wake Slyvester Namiwa atuluke mchitokosi.

Mneneri wa CDEDI Promise Thom wati apolisi asunga a Namiwa kwa masiku 4 popanda mlandu uliwonse ndipo lero akuyenera kudziwa chomwe analakwa.

Thom wati owayimira pa mlandu a Namiwa ali tcheru kuti atsate njira zoyenera komanso kupempha kuti atuluke pa belo.

Iwo atsindika kuti CDEDI siphethira ndipo lipitiriza kuunikira momwe adindo akugwirira ntchito yawo mdziko muno.

Thom wati iwo ndi othokoza kwa magulu onse omwe ayima nawo pa nthawiyi.

Wolemba: Jane Chirwa -Lilongwe

 Matimu a Ekhaya FC ndi Mighty Wanderers ndi amene akumane mu mdime yotsiriza ya chikho cha Airtel Top 8 chaka chino. Ti...
03/08/2026



Matimu a Ekhaya FC ndi Mighty Wanderers ndi amene akumane mu mdime yotsiriza ya chikho cha Airtel Top 8 chaka chino.

Timu ya Ekhaya FC yafika mu mndimeyi itagonjetsa timu ya Karonga United ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi pa 1 August 2026 pabwalo la Silver.

Mighty Wanderers yagonjetsa timu ya Blue Eagles 5-4 kudzera mndime ya mapenote masewerawa atethera kufanana mphavu 1-1 pa mphindi 90 masewero omwe anali Lamulungu pa 2 August pabwalo la Silver.

Matimuwa akuyembekezeka kuzakumana kumathero amwezi uno pa 29 August 2026.

Wolemba:Noel Mtanga- Lilongwe(3/8/2026).

  Timu ya Scorchers yangochetsa timu ya Egypt women ndi zigoli zitatu kwa chimodziMasewerowa   anachitikira  pa bwalo la...
01/08/2026




Timu ya Scorchers yangochetsa timu ya Egypt women ndi zigoli zitatu kwa chimodzi

Masewerowa anachitikira pa bwalo la Rabat Stadium dziko la Morocco.

Awa ndi masewero a chiwiri a timu ya Scorchers kupeza chipambano.

M'mene zatelemu timu ya Scorchers ili ndi pointi 6.

Egypt women 1 - Scorchers (Malawi Women) 3

Wolemba Iqra Adani - Mangochi

Address

Area 24
Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when We Can Media Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to We Can Media Online:

Shortcuts

Share