Ticia's daily life

Ticia's daily life Kucheza kudziwitsana ndiku phunzitsana

Ukuoneka kumeneko mweziwo
07/09/2025

Ukuoneka kumeneko mweziwo

  Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha uzimu yemwe anali mzika ya dziko la Rwanda Gloriose Musabyimana, yemwenso amadziw...
04/09/2025



Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha uzimu yemwe anali mzika ya dziko la Rwanda Gloriose Musabyimana, yemwenso amadziwika ndi dzina loti Gogo, watisiya ali ndi zaka 36.

Imfa ya katswiriyu yatsimikizidwa ndi mneneri wake, Bikem wa Yesu, yemwe anali naye limodzi m’dziko la Uganda komwe amakayimba koma anayamba kudwala mwadzidzidzi.

Kuno ku Malawi anthu ambiri anamudziwa oyimbayu chifukwa cha kanema wa nyimbo yake yotchedwa “ Every Day I need Blood of Jesus” yomwe anayiyimba mopatsa chidwi ndi mawu ake a nthetemya ndipo anthu anayigawana kwambiri kudzera pa masamba a mchezo.

Iye anabadwa mchaka cha 1989 m’dera la Rwamagana mdziko la Rwanda. Katswiriyu, yemwe anali wa mpingo wa Anglican, anakula ngati mwana wa masiye pomwe makolo ake onse anamwalira ali wachichepere.

Olemba: Simeon Boyce

Mwadzuka bwanji anthu okongola inu amene mukuwaona apawa ndi a Teresa Mutale aku Zambia, leroli akukapangidwa surgery (o...
04/09/2025

Mwadzuka bwanji anthu okongola inu amene mukuwaona apawa ndi a Teresa Mutale aku Zambia, leroli akukapangidwa surgery (operation) tiyeni tiwafunire mafuno abwino komanso tiwaikize mmapemphero mu umodz muli mphamvu 🙏❤️

Good morning beautiful people this is Mum Teresa Mutale from Zambia and she is set for a surgery today let’s wish her well and pray for her successful Surgery 🙏❤️

  Kafukufuku wina watsopano wapeza kuti kudya tchipisi katatu kapena kupyola apo pa sabata kumayika kwambiri anthu pa ch...
07/08/2025



Kafukufuku wina watsopano wapeza kuti kudya tchipisi katatu kapena kupyola apo pa sabata kumayika kwambiri anthu pa chiopsyezo cha matenda a shuga.

Malingana ndi akatswiri azakafukufuku pa sukulu yaukachejede ya Cambridge ku England, anthu omwe amadya tchipisi katatu pa sabata olo kupitilira apo, ali pa chiopsyezo chachikulu cha matenda a shuga kusiyana ndi omwe amadya mbatatesi yootcha kapena yowilitsa.

Dotolo wina wa bungwe loona za matenda a shuga ku England, Dr Riley, wati kafuku fukuyo waonetseratu poyera kuti kaphikidwe kachakudya kamatha kupereka chiopsyezo chokhuza matendawa.

Olemba: George Banda

Brenda Tioneso wapezeka atafa mnyumba yake Ku nsanje koma chitseko chosathyola . Iye wabwera kumene kuchokela kujoniwail...
25/07/2025

Brenda Tioneso wapezeka atafa mnyumba yake Ku nsanje koma chitseko chosathyola . Iye wabwera kumene kuchokela kujoni

wailesi ya MIJ yalemba kuti atafika anapeza kuti Mwamuna Waka anakwatilanso mkazi wina ndipo anayamba kupanga za divorce kuti Banja lithe .

Masiku ochepa apezeka atafa mumutu Mwake mukuoneka mabala.

source : MIJ FM

 Apolisi ku Lilongwe amanga anthu atatu omwe akuwaganizira kuti akhala akuchita za uchifwamba zosiyanasiyana ndikupha an...
21/07/2025


Apolisi ku Lilongwe amanga anthu atatu omwe akuwaganizira kuti akhala akuchita za uchifwamba zosiyanasiyana ndikupha anthu ku Area 25.

Mneneri wapolisi mdziko lino a Peter Kalaya watsimikiza kuti atatuwa ndi a Dyson Sinedi omwe akuti anawamanga ku area 43 komanso a Adam Tsoka ndi a Felix Magaleta omwe akuti anawamanga kwa Mgona kumapeto asabatayi.

Pakadali pano apolisi akuyenda ndi anthuwa m'malo momwe amachita zachiwembuzi pomwe akufotokoza momwe amachitira izi.

Anthuwo akuti amayenda pa njinga ya moto ndipo amagwiritsa ntchito chitsulo kumenya anthu.

Kuyambira mwezi wa May, nkhani za uchifwamba 13 ndizo apolisi akuti zachitika ku Aarea 25 ndipo anthu asanu afa atawamenya.

(by John-Paul Kayuni - Lilongwe: 07/21/25)

 A Egnat Katengeza omwe akuganizilidwa kuti anatengapo gawo pa imfa ya a Agnes Katengeza, aja anali mkulu owona za Netiw...
17/07/2025


A Egnat Katengeza omwe akuganizilidwa kuti anatengapo gawo pa imfa ya a Agnes Katengeza, aja anali mkulu owona za Netiweki ku Reserve Bank of Malawi, akuwasunga ku ndende ya amayi ya Kachere mu mzinda wa Lilongwe.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu wati izi ndi kaamba kakuti apolisi akumalizitsa ndondomeko zina za mlanduwu asanawutengere mkhothi.

Apolisi akuyembekezeka kutengera mayiyu ku Khothi mtsogolomu akamaliza ndondomekozi.

A Egnat Katengeza anali mchemwali wawo yekhayo wa mayi ndi bambo amodzi wa a Agnes Katengeza, ndipo iwo ndi munthu wachiwiri kumangidwa pa nkhaniyi, kuphatikizapo mchimwene wa a Agnes, Amos Katengeza.

A Agnes Katengeza anapezeka atafa mgalimoto la ku ntchito kwawo kuseri kwa Gateway Mall mu September, 2023.

(by Innocent Kumchedwa -Lilongwe;07/16/25)
Copied from ZBSnews

16/07/2025

WHY ALWAYS AREA 25 LILONGWE?💔😭🕊️
Apolisi ku Lilongwe amanga a Egnat Katengeza azaka 51, omwe ndi mchemwali wawo yekhayo wa mayi m'modzi ndi bambo amodzi wa a Agnes Katengeza, aja adali mkulu owona za netiweki ku Reserve Bank of Malawi, kuti akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa mchemwali wawoyu mchaka cha 2023.

A Katengeza anapezeka atafa kuseri kwa Gateway Mall mu mwezi wa September, 2023, ndipo apolisi anamanga mchimwene wawo a Amos Katengeza. Malingana ndi mneneri wa polisi ku Lilongwe a Hastings Chigulu, a Amos anatchula a Egnat kuti anatengapo gawo lalikulu pa imfa ya a Agnes.

Malingana ndi apolisiwa pa nthawiyo apolisi adawayitanitsa a Egnat, kukawafunsa mafunso ndipo kumangidwa kwawo kukutsatira kafukufuku yemwe wakhala akuchitika.

Iwo atinso a Egnat Katengeza ndiwo adali munthu woyamba kukachita lipoti za kusowa kwa mchemwali wawo tsiku lomwe anapezeka atafa. Mayiyu yemwe ndiwaku Area 25 amutsegulira mlandu wakupha.

Gogo otchuka kwambiri ndi kuthamanga, Fauja Singh, wamwalira ali ndi dzaka 114.Fauja, anayamba olympic running ali ndi d...
15/07/2025

Gogo otchuka kwambiri ndi kuthamanga, Fauja Singh, wamwalira ali ndi dzaka 114.

Fauja, anayamba olympic running ali ndi dzaka 89, amalimbikira mpaka anapatsidwa dzina loti 'Turbaned Tornado' ndipo amathamangabe.

Monday pa 14 July, Fauja anagundidwa ndi galimoto nkumwalira.

UTHENGA WACHISONI MMAWA UNO💔Very Sad Zachitika ku Chilomoni💔💔💔William Makwangwala yemwe ali pachithunziyu akuti kwawo ku...
10/07/2025

UTHENGA WACHISONI MMAWA UNO💔

Very Sad Zachitika ku Chilomoni💔💔💔

William Makwangwala yemwe ali pachithunziyu akuti kwawo kunabwera wakuba, pothamangitsa wakubayo anamuona akulowa ku plot yoyandikana nayo ndiye anapitako kukafumsa ngati sanaone munthu wachilendo atathawira kumeneko iye anafotokoza kuti akuthamangitsa wakuba anabwera kwawoko koma wathawira kumeneko atangotero kuyankha kunamvuta mnyamata ofunsidwayo ndipo pompo anatulutsa mpeni nkubaya pamimba💔💔 Mnyamata wabaya nzakeyo akuti ndi Doxxy dzina lake

AnamanAnamandwa

Komwe ku Chikwawa pa Malo amene anthu okhala kwa Thendo amadzayima pa malopa kumasaka netiweki ya foni akafuna kuyimba.K...
01/07/2025

Komwe ku Chikwawa pa Malo amene anthu okhala kwa Thendo amadzayima pa malopa kumasaka netiweki ya foni akafuna kuyimba.

Kumakhala kumverana nkhani apa

Address

Lilongwe

Telephone

+265981778984

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ticia's daily life posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share