
30/07/2024
Official Music Video
https://youtu.be/NX2qVwPKHNI?si=39rXzlJ3jx6EonjT
‼️‼️‼️IZIZI SI ZA INE KOMA ATELO YEHOVA WAKUNVA ANVE‼️‼️‼️👇
Pali denga pamutu pako
Winawake cha dela lomwelo wagona k**i kwa buliji,
Koma mukudandaula kuti mumagona pansi.
Winawake sanadye lelo lose, iwe ukudandaula kuti sunadyere ndiwo zabwino.
Bola inu muli Ndi chofunda anzanu alibiletu akungwa Ndi Mphepo kunjako.
Simumayamika Yehova ndiye akusamala inu osati kuthekela kwanu.
Za abale amene mulinawo
Zoti kukhala Ndi banja Ndi chithu chosowa Ndi chantengo wake wapatali
Inuyo simumaziona zofunikira.
Anzanu amalakalaka akanakhala Ndi makolo awo tikunena lelolino,
Akakhalakhala amangolingalira
Amayi, Bambo wawo chikhala nthawi imabwelela akadakawatenga azidzakhala nawo ntsogololi tsopanoli.
Ana mukutayawo, simmene kholo lina likukwelela mapiri kuti akhale naye wawo mwana.
Zimathela muntima
Misonzi yosaleka
Anthu osweka mitima
Kupinda mawondo awo usana Ndi usiku kufuula kwa Yehova
Aliko anthu ena akupembedzadi muchoona. Mukudandaula kuti mukugwira nthyito yomwe siyomwe munkailota kubwana kwanu , simuli okondwa Ndi malipiro omwe mumalipidwa , ena sanaiwonepo ngakhale amalakalaka nthyito mukuipsyayo akuisowa.
Simukhutitsidwa Ndi phindu lomwe mumapeza pa malonda amene mumachita chosecho mukukwanitsa kudyetsa Ndi kukhutitsa mimba zanu pa mdalitso omwewo omwe anzanu akuwusowa, aliko ena amalakalaka akanakhala nawo mpamba oyambila geni koma sanaupeze
Komatu inu simuli akuyamika.
Aliko kunjako anzanu akufunafuna Yehova pamene akupezeka iye munzimu Ndi mu choonadi
Zolemetsa Ndi ziphinjo akumana nazo koma ali chilimbile kukhulupilira Yehova
Ndiwo opembedza mu choonadi.
Chomwe ulinacho iwe lelo wina alibe koma sukhuta ukumakakhumbilaso za wina
Anthu akusawelezika inu Ndi adyera
Mulibe kuyamika
Mizimu yosathokoza inu
Mukadalinayo njala yongokhumbabe zapansi pano koma simudzakhuta.
Pakuti zikhumbo zanu ndi zilakolako zanu zikukutengelani kuchionongeko
Koma simudzuka ku tulo tanu.{finish comment section}