
10/09/2025
Anthu ochokera m'dera la Mitundu m'boma la Lilongwe ati ndi okhutila ndimomwe gawo la chiwiri lomanga nyumba za makono zokhala ndi ma computer (ICT Labs) msukulu za sekondale ndi pulayimale layambira pa Mlomba CDSS.
Ntchitoyi inakhadzikitsidwa ndi bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) kudzera mu komiti ya Universal Service Fund (USF).
Malingana ndi wapampando wa komiti ya Universal Service Fund ( USF) a Manyanda Nyasulu ati cholinga cha pulojekiti ya "Connect A School", ndi kupititsa patsogolo maphunziro mdziko muno powapatsa ana a sukulu danga logwiritsa ntchito ma computer komanso makina a internet.
Nyumba za Makonozi (ICT Labs) zili ndi kuthekera kosunga ma computer okwana 60 . Nawo anthu ozungulira sukulu ya Mlomba CDSS adzakhala ndi mwayi ogwiritsa ntchito makina a internet mwa ulele ngati ali pafupi ndi sukuluyi maka maka pa mtunda osapitilila 200 mitazi.
Pofuna kukwaniritsa masomphenya a Malawi 2063, Bungwe la MACRA mu gawo lachiwiri la pulojekiti ya Connect A School lati Nyumba za Makono za ma computer ( ICT Labs) zokwana 120 zimangidwa m'madera osiyanasiyana mdziko muno.
Mu gawo loyamba, Nyumba za Makono za ma computer (ICT Labs) zokwana 75 zamangidwa kale m'madera osiyanasiyana ndipo ziyamba kugwira ntchito posachedwapa.
Kudzera mu Ntchito yomanga nyumba za makono za ma computer (ICT Labs ) mu pulojekiti ya "Connect A School" , anthu ambiri apeza mwayi wa ntchito komanso bizinesi mu derali.
Olemba: Joseph Chibade