05/05/2026
kudziko kuno kuli Chida chodziwika bwino kwambiri choletsa kugwiriridwa ndipo dzina lake ndi Rape-aXe (chomwe chimatchedwanso Rapex),chidachi chidapangidwa ndi ndi Dr. Sonnet Ehlers mu 2005 ku South Africa.Chidachi chili ndi mano kapena kuti mizere yakuthwa kwambiri ndipo chimavalidwa kumalo obisika a mkazi ngati mene imakhalila kondomu yachikazi. Ngati mamuna akulowetsa,Mano aja amamangirira pa Chida cha mamunayo, zomwe zimapweteka kwambiri ndipo zimamulembalemba. Chipangizochi chimakakamila ku Chida cha mamunayo ndipo chimachotsedwa munjira ya opaleshoni yachipatala yokha basi, zomwe zingathandize kuzindikira wogwiririra ngati afuna chithandizo.
Ngakhale kuti chipangizochi chidakopa chidwi cha anthu ambiri padziko lonse, sizidapangidwe zochuluka kapena kugulitsidwa pamsika chifukwa anthu ena komanso omenyera ufulu akhala akutsutsa zachidachi pakuti kusazitenga bwino zikhonza kuzetsa Imfa Kwa ogwilirayo.
Akatswiri ena adati ndibwino tilimbane ndi zomwe zimayambitsa nkhanza yogwilira osati kupanga chidwa chimene chili chopweteka anthu.
Ngakhale Dr. Ehlers adakonza zopanga komanso kugawa zidazi zokwana 30,000 pa FIFA World Cup ya 2010, kusowa kwa ndalama ndi mikangano pakagwilidwe ntchito kake kudasokoneza ntchitoyi
Maganizo Anu ndi otani pankhaniyi, kayambe kugwira ntchito kapena ?