03/08/2025
NDAKUPATSA
Sendera pafupi Namwaliwe, ndikuthere mawu.
M'mene ndikuti ndimakukondamu usayese mabindi.
Sinthabwala zoti ndimakusowa mphindi iliyosee.
Nzenizeni zochokera pansi pa Mtima.
Undikhulupilire, Sindingakugwilitse fuwa lamoto.
Ine apa ndikulumbira!! Misozi sindidzakutulutsitsa,
Apo biii!! Idzakhala yachimwemwe.
Chabwino mutu wa Yohane m'batizi mudzadule pokwanisa lonjezo.
Undivetsere bwino Bwino zomwe ndikunena.
Umandimaliza,,,Umandidolora.
MOTi thupi langa lonse limachita tsembwe ukandiyang'ana.
Nanji ukandisekelera??
Ubongo wanga umasiya kuganiza.
Mwazi wanthupi langa umatentha kuti juuuu!!
Ukumwazika mosochera m'misempha.
Ndiye basi ndakupatsa Ntimawu.
Uwuchengetere ngati mandanda.
Eko Tenga Nkhokwe yachikondi changa chozama.
Ndakupatsanso Nthawi yanga yonse,
Zilumika zodzasamilana pachidale tikutchulana:
sweetie 💕 dear ndiso darling mpaka kukalambirana.
Ulipotu wekha dziwa
Palibenso angamake khalidwe ndikukongola kwako.
Kadya nkena mbiri ndiyakhoswe inde.
Koma dziwa alidere nkulinga utayenda naye.
Poti ine sindili ngati amaliongo,
Ongomuvura Nkazi basi akatero athana naye,
Ongodziwa kuswa mitima nkusiya chiphadzuwa chikulira😭.
MOTi ndimadzifusa kuti zoona akanganyawa akuseweletsa duwa🌹??
Koma amadziwa mmene zimavekera ??
Mpake ndabwera kudzatolera kudzasonkhanitsa tizidutswa tantima oswekawo,
Chifukwa ndikudziwa kuti nthiti yomwe adapangira iwe ndiyanga.