03/02/2025
Mphenzi updates
A Bonface Ofesi sazaka 25 afa ataombedwa ndi mphezi lero m'boma la Ntchisi.
M'neneri pa polisi ya Ntchisi a Salomy Zgambo, ati ngoziyi ya chitika pa mudzi otchedwa Kaphatiye m'bomalo.
Iye wati wati pa nthawiyo, malemuwa amalima m'munda mwao koma mwadzidzi mvula ya mphamvu inayamba komanso kuti pa nthawi yomwe amafuna adzithawa mpheziyo inawamenya ndikuwatentheranso zovala zonse.
Pakadali pano, ofalitsa nkhani pa chipatala chachikulu cha m'bomalo a Frank Kaphaso ati a Bonface afa kamba koti adatenthedwa kwambiri ndi moto wa mpheziyo.
A Bonface, amkachokera pa mudzi wa chimwankhuku ku dera la mfumu yaikulu Malenga m'bomalo.
(by Thokozani Namuku-Ntchisi:02/03/2025)