Tione Tv

Tione Tv Nkhani Kwa Inu

07/11/2023

UNIVERSITY YAKANA NAMADINGO, MPHANDE NDI SHARIF KARIM

Sukulu ya ukachenjede ya South Africa yakana kuti Namadingo, Pemphero Mphande komaso Mansoor Sharif Karim analandila ma degree a udotolo ku sukuluyi.

Muchikalata chomwe sukuluyi yatulutsa anthuwa akanidwa kuti siyikuwadziwa ndipo sanakhalepo ndimayina awo ngati ophunzira apa sukuluyi.

Izi zachitika masiku ochepa chabe a Pemphero Mphande atatulutsa zithunzi patsamba la m'chezo kuti apatsidwa degree ya udotolo ndi sukuluyi.

Tione Tv
01/11/2023

07/11/2023

CHAKWERA AKUPITA KUNJA

President Chakwera akunyamuka kupita ku Saudi Arabia komaso ku Egypt mawa. Nduna yofalitsa nkhani a Kunkuyu atsimikiza za nkhaniyi.

Chakwera akakumana ndi akatakwe ndi mankhumutcha ku Saudi Arabia komaso Egypt ndikukambilana nawo nkhani za ulimi, chitukuko komaso zachuma kuno ku Malawi.

Tione Tv
07/11/2023

07/11/2023

NORMAN CHISALE WATI BOMA LIKUMUZUZA

M'modzi wa a silikari omuteteza president wakale a Norman Chisale wakamba kuti boma la Tonse Alliance likumuzuza kwambiri.

A Chisale omwe anamangidwa kangapo m'mbuyomu powaganizila milandu ingapo ati sanamangidwe motsata malamulo.

Mu interview yomwe anachita ndi Zodiak ati iwo komaso Chilima ndi Bushiri akuzuzidwa ndi boma chifukwa amachokela ku Ntcheu.

Tione Tv

06/11/2023

NTHENDA YA CHIKUKU YABUKA KU LILONGWE

Matenda a chikuku a buka ku area 36 mu mzinda wa Lilongwe. Unduna wa za umoyo watsimikiza kuti anthu 14 apezeka ndi nthendayi atawayeza ndipo onse ndi ana osapitilira zaka 15.

Pakali pano undunawu wati ukupeleka katemela kwa ana onse m'madela omwe akuwaganizila kuti nthendayi ithakufala ngati njira imodzi yopewela nthendayi.

Tione Tv

06/11/2023

CHILIMA WATI SIOPUSA

Mtsogoleri wachiwili wa dziko Dr Chilima wati siopusa pamene wakhala chete kwa nthawi yayitali. Pa kanema yemwe akuyenda pama samba a mchenzo.

A Chilima ati akhala akudikila nthawi Yoyikika kuti ayankhule zomwe zili kukhosi kwawo. Mukuyakhula kwawo ati week YAMAWA akhala ayakhula bwino bwino patatenga nthawi yayitali osayankhula.

Tione Tv

06/11/2023

BULLETS Vs WANDERERS 1-1

Pa masewero a mpira wa miyendo matimu a Mighty Mukuru Wanderers komaso FCB Nyasa Big Bullets alephela kutulutsa owina masewerowa atathera 1-1.

Kulephalanaku kwapangitsa matimu awiriwa kukhala ndima points ofana omwe ndi 54 points ngakhale Bullets ikutsogola ndizigoli. Mu table yampikisanowu Bullets ya sewera ma game okwana 25 pomwe Wanderers yasewera ma game okwana 28.

Tione Tv

05/11/2023

AFUKULA MALIRO OYIKIDWA KALE

A police mogwilizana ndi mafumu ku Mulanje apeleka chiganizo choti maliro omwe anayikidwa pakhomo la munthu akachotsedwepo.

M'maweek angapo apitawa a Gloria Chipungu ochokera m'mudzi wa a Mayero ku Mulanje anakaniza kuti maliro ayikidwa kumanda kamba koti mandawo amasunthira kumalo awo. Zotsatila zake anthu okwiya anakayika malirowa pakhomo lawo.

Malawi Police mogwilizana ndi mafumu akukuluku aku Mulanje akachotsa thupilo ndikukayika kumanda monga momwe zimayenela kukhalira.

Tione Tv

04/11/2023

PROF JOHN CHISI ALOWA MCP

M'modzi mwa anthu andale otchuka ku Malawi a Prof John Chisi alowa Chipani cha MCP. A Chisi omwe analiso President wa chipani cha Umodzi Party atuluka chipani chawo ndikulowa MCP.

Iwo ati akufuna Kugwira ntchito ndi President Chakwera kamba koti Ali ndi masophenya abwino otukula Malawi.

Tione Tv

04/11/2023

Takulandilani pa Tione Tv Kubweletsa nkhani zosiyanasiyana zochitika ku Malawi. Tikubweletsa ma episode kapena kuti kanema ozukuta zomwe zikuchika ku Malawi tsiku lili lonse komaso nkhani mwachidule tsiku lili lonse. Tipangeni follow kuti zisakuphonyeni aMalawi.

Zikomo

Address

Lilongwe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Tione Tv posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Tione Tv:

Share

Category