05/02/2025
KUBA MOWA POOPHSYEZA NDI MFUTI
Paul Dominic wazaka 22 yemwe amachokera kwa Safarao, mfumu yaikulu Kapena ku Blantyre ali m'manja mwa apolisi pomuganizira kuti wapezeka ndi mfuti popanda chilolezo yomwe anagwiritsi ntchito pofuna kuba laundi ya mowa poophyseza ogulitsa.
Mneneri wapolisi ya Ndirande, Maxwell Jailosi walongosola kuti Dominic anapita pamalo ena omwera mowa otchedwa Nyozani kwa Safarao ku Ndirande komweko komwe amapanga chinkondwa ndi mzake wina poitanitsa mowa wankhani-nkhani.
Koma pamene Dominic anakuwanso kuuza ogulitsa kuti amupatse mowa wina, ogulitsa uja anauza mbiyan'gambeyi kuti iyambe kaye yalipira ndalama za mowa omwe wamwedwa kale.
Izi zinakwiyitsa Dominic kwambiri ndipo anatulutsa mfuti nkumulodzetsa ogulitsayo uku akumuuza kuti "iwe ndipatse mowa wina, kupanda kutero ndikuombera".
Ogulitsayo sanachitire mwina koma kukuwa kuti ena amuthandize.
Thandizolo linabweradi kuchokera kwa anthu ena omwe amamwa mowa pamalopo omwe anagwira Dominic nkumuvumbitsa nazo zibakela.
Mzake was Dominic ataona kuti kwavuta iye anaonetsa kunsi kwaphazi, kuthawa.
Pakadali pano, Dominic ali mmanja mwa apolisi ndipo mfutiyo amulanda.