Mwaluwazi family

Mwaluwazi family Born 05/02/1967 at Embangweni in Mzimba District, Malawi. Attended primary school education at Embangweni Full Primary School.

I further attended Secondary Education at Kongwe ( Robert Blake
Sec.School).College Education at Kasungu TTC.

09/04/2026
10/08/2025

Anthu tili ndi mavuto ambiri mmene timaganizila. Ife amene tinabadwa nthawi ya ulamuliro wa Dr H. Kamuzu Banda ngati mukukumbukila timakhala mu ulamuliro okhala mwa mantha kwambiri. Manthawo amabwera poopa anthu olamulira osati munthu wamba. Zophana kudalibe chifukwa anthu timaopa malamulo.

"You've got to get up every morning with determination if you're going to bed with satisfaction."
04/08/2025

"You've got to get up every morning with determination if you're going to bed with satisfaction."

Ndinenepo za ndaleA professor Peter Arthur Mtalika nawo atatenga Boma la Malawi adalipeza Lili kale pa mavuto omwe adawa...
28/07/2025

Ndinenepo za ndale
A professor Peter Arthur Mtalika nawo atatenga Boma la Malawi adalipeza Lili kale pa mavuto omwe adawasiya a Joice Banda. Komabe iwoso adayetsetsa kuti aliwongolere dziko lino kuti likhale lozidalira pa chuma koma zinthu sizidasinthe olo pang'ono mpomwe ndiye anthu a mdziko muno sadawakhululupibe moti nthawi ya mavoti itakwana, anthu anayamba kutaya chikhulupiliro ndikuvotela a Lazarus Chakwela yemwe anthu adamukhulupilira kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino pa ndale, chuma, Zaumoyo, maphunzilo komanso za ulimi ndi zina zambiri.

Ndinepo nkhani za ndalePart 2Atamwalira a Bingu Wamtalika potsatila malamulo a dziko lino amayi Joice Banda adazonzedwa ...
28/07/2025

Ndinepo nkhani za ndale
Part 2
Atamwalira a Bingu Wamtalika potsatila malamulo a dziko lino amayi Joice Banda adazonzedwa kukhala pulezidenti wa dziko lino.Iwowa adapitiliza kuyendetsa dzikoli lili pa mavuto opitilira muyeso komabe adayetsetsa kuwongolera kwinako akutukwanidwa ndi a Malawi ngati muja zidakhalira mu Baibulo nthawi ya utsogoleri wa Mose kupita ku Kenani. Mwamwayi iwowa adakafika mpaka kumalizitsa zaka zotsala zomwe adazisiya malemu Bingu Wamtalika. Mwatsoka, chifukwa cha mavuto omwe adafika poyipa kwambiri pa nkhani ya zachuma chomwecho anthu sadawavotele kukhala mtsogoleri wa dziko. Masomphenya aanthu adali asanakwanilitsidwe molingana ndi mmene anthu amafunila.Iwowa sadapanilire mpando koma kuusiya mmanja mwa Professor Peter Arthur Mtalika amene ndi mchimwene wawo wa malemu Bingu.Tikawona modekha, titha kuvomeleza kuti iwonso adayetsetsa mbali yawo ngati mtsogoleri wokonda dziko lawo koma lochulukaso anthu alibela Boma chuma chomwe chidali chochepa kukwanilitsa kuthetsa mavuto.

28/07/2025

Tikambeko za ndale 🤩
Kwa ife tinabadwa nthawi ya Dr H. Kamuzu Banda ndili ndi chikhulupiliro kuti timatha kusiyanitsa bwinobwino mmene zinthu zimakhalira matsiku amenewo tikulamulidwa ndi chipani chimodzi. Tikatembenuza mbali inayi ya Multi Party Democracy takhala tikutsatila kuona zipatso zomwe zinabwera ndi olamula onse kuyambira a Bakili Muluzi kufikila a Dr Lazarus Chakwela.A Muluzi adali ndi zokoma zambiri koma zowawa nazo zidalipo malingana ndi mavuto a mgonagona imwe dziko lino limakumana nawo monga achilengedwe komanso ena ochita kukonza akuluakulu olamula monga katangale, kusankhana mitundu polemba a ntchito mu boma komanso mu ma bungwe odziiyimila pa okha.Kufooka kumeneko anthu a mdziko muno sadataye chiyembekezo koma kupereka danga lina kudikila ndi chiyembekezo kuti mwina zinthu zizasintha kukomela wina aliyense mdziko muno.Mbali yawo adayetsetsa mwina ndi mwina. Mwachitsanzo lero tili ndi ma lamya mmanjawa, ma TV, ufulu olemba ngati mmene ndikulemberamu ndi zina zambiri. Atachoka nthawi yawo itakwana akuluakulu amene amakhala nawo pafupi ndikumasangalala kulamulira adaona kuti ndibwino abwanawo apitilize kulamulira mosemphana ndi malamulo a dziko lino pofuna kulowetsa third term bill.Chilakolako chofuna kumadyelera ndithu pamene anthu a kumudzi samadyelera nawo.Izi zidalephereka ku nyumba ya malamulo pomwe aphungu ochuluka sadavomeleze.Mmalo mwake iwo adasankha Bingu Wamtalika munthu wamasomphenya ndiponso okonda dziko lathu la Malawi.A Bingu adali munthu wolimbika kwambiri ngakhale kuti adakumana ndi mavuto oposa a zachuma moti iwowo poti adakonza kuti ndibwino a Malawi azunzike kwa kanthawi koma adzakhale akusangalala patsogolo pake ngati mmene tonse yikudziwila kuti munthu ayenela kuti adutse kaye muzokhoma kuti kuwala kubwere.Nkhaniyi idakhumudwitsa a Malawi ambiri ndipo mothandizidwa ndi azipani zotsutsa a Bingu adanyozedwa paliponse ngati munthu opanda nzeru. Mwa tsoka, a Bingu adatengedwa ndi Mulungu. Mzimu wawo uziusa m'mtendere.Ndipitiliza 😊

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mwaluwazi family posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share