GBS Your Family TV

GBS Your Family TV GBS Your Family TV: Your go-to destination for wholesome entertainment. Discover shows and programs that make family time special.

 ‎‎Mt'sogeleri wa Democratic Progressive Party-DPP Professor Arthur Peter Mutharika ndi wachiwiri wawo Dr Jane Ansah ndi...
24/09/2025



‎Mt'sogeleri wa Democratic Progressive Party-DPP Professor Arthur Peter Mutharika ndi wachiwiri wawo Dr Jane Ansah ndi omwe apamba pachisankho cha pa 16 September 2025.

‎Malingana ndi nkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission-MEC Justice Annabel Mtalimanja walengeza kuti a Professor Muntharika apambana ndi mavoti 3,035,244 Miliyoni (56.8%) pamene yemwe anali tsogoleri wakale wadziko lino komaso wa Malawi Congress party-MCP Dr. Lazarus Chakwera apeza mavoti 1,765,170 Miliyoni (33.0%).

‎Professor Arthur Peter Muntharika angonjetsa atsogoleri 16 azipani zina komaso oyima pawokha omwe anatenga nawo mbari pachisankhochi.

‎Zatelemu a Muntharika omwe anakhalaponso ngati m'tsogoleri mzaka za 2016 kufikira 2020 akuyenera kulumbiritsidwa pakatha masiku 7 owulutsa ndi kusapitilira masiku 31 owulitsira zotsatira zachisankho.


‎(Wolemba Thom Kamanga)

 ‎‎Chipinda chomwe bungwe la Malawi Electoral Commission-MEC likufuna kulengezetsa zotsatira za chisankho cha m'tsogoler...
24/09/2025



‎Chipinda chomwe bungwe la Malawi Electoral Commission-MEC likufuna kulengezetsa zotsatira za chisankho cha m'tsogoleri chadzadza tsopano ndi anthu osiyanasiyana kudira komishoni ya MEC kuti ifike.

‎Kupatula nyumba zoulutsa mawu ziri muchpindamu, pa malowa pafikanso, mthumwi zoyang'anira chisankho zakunja komaso zakuno ku Malawi, akuluakulu achitetezo ndi atsogoleri amabungwe.

‎Lero ndi tsiku lomwe mtundu wa aMalawi maso ake onse ali ku Bingu International Convention center (BICC) komwe nkulu wa MEC Justice Annabel Mtalimanja akuyembekezeka ku lengeza yemwe wapambana ngati m'tsogoleri wadziko lino pachisankho cha pa 16 September.

‎(Wolemba Thom Kamanga)

 Business is at stand still within Lilongwe City Centre as shops and offices are closed, a move to avoid chaores that mi...
24/09/2025



Business is at stand still within Lilongwe City Centre as shops and offices are closed, a move to avoid chaores that might arise as MEC is expected to announce the winner in the 2025 Presidential Election race.

‎In the streets few people are seen moving up and down mainly DPP supporters going to join fellow members gather near Parliament building awaiting for the announcement tonight.

‎Currently, there is tight security with deployment of MDF solders and Malawi Police officers in some places within the city.

‎There has been fears of riots as the tension was so high that followers of other political parties that lost the election will not concede the defeat.

‎Malawi Electoral Commission (MEC) through it's chair, Justice Annabel Mtalimanja, is poised to declare DPP torch bearer, Professor Arthur Peter Muntharika winner, as he is leading the race with over 2 million votes followed by MCP's Dr Lazarus Chakwera who amass about eight (8) hundred thousand votes.

Earlier in the day, Dr. Chakwera conceded defeat and congratulated Prof. Mutharika.

‎By Thom Kamanga

 ‎‎Bungwe la Civil Society Elections Forum, CSEIF lati ndilokonzeka kugwira ntchito modzipereka ndi boma la tsopano lomw...
24/09/2025



‎Bungwe la Civil Society Elections Forum, CSEIF lati ndilokonzeka kugwira ntchito modzipereka ndi boma la tsopano lomwe likuyembekezera kutsogozedwa ndi Professor Arthur at Peter Mutharika.

‎Bungweri lanena izi kudzera mwa wachiwiri kwa wa pampando Gift Trapence yemwe wayamikira a Malawi posonyeza ufulu wa demokalase komanso kusunga bata mu nyengo yoyembekezera zotsatira zotsimikizika ndi bungwe la MEC.

‎CSEIF lafotokozaso kuti lawona mavuto ena monga kuvuta kwa kutumiza zotsatira kuchoka m'ma dera ovotera kupita ku likulu la MEC ndipo alonjezanso kuti akhala akupanga mikumano ndi akuluakulu a MEC ndi cholinga chofuna kusintha malamuro ena omwe amalepheretsa maguru ena ngati atolankhani, ogwira ntchito ku MEC ndi olumara kuponya voti.

‎Trapence watinso kukhala kofunika kuti boma la tsopano kuti liike zilango zokhwima zokhaulitsira zipani zomwe zimafuna kusokoneza chisankho.

‎Wolemba : Jamie Michael
‎Wojambula : Thom Kamanga

 ‎‎Anthu otsatira chipani cha DPP ayamba kusokhana panja pafupi ndi komwe akuyembekezela kulengeza zotsatira zachisankho...
24/09/2025



‎Anthu otsatira chipani cha DPP ayamba kusokhana panja pafupi ndi komwe akuyembekezela kulengeza zotsatira zachisankhoku BICC.

‎Achilikari akhondo komaso apolisi akhala atseka mbari zonse zolowera ku malowa ngati mbari imodzi yopeleka chitetezo.

‎(Wolemba Thom Kamanga)

 ‎‎Bungwe loyendetsa chisankho dziko la MEC la sintha nthawi yochititsa msokhano wake wofuna kulengeza zotsatira zachisa...
24/09/2025



‎Bungwe loyendetsa chisankho dziko la MEC la sintha nthawi yochititsa msokhano wake wofuna kulengeza zotsatira zachisankho kuchokera 2 Koloko masana kupita usiku walero.

‎Malingana ndi m'neneli wa MEC a Sangwani Mwafuliwa ati kusithaku kwadza kaamba koti pali madandu ena omwe bungweri likufuna kukonzelatu lisanabwere ndi zotsatira kutengera ndi malamulo oyendetsera chisankho akunenera.

‎Ngakhale pali kusithaku, a Mwafuliwa sanafotokonze nthawi yeni yeni yolengeza zotsatirazi.


‎(Wolemba Thom Kamanga)

 ‎‎BREAKING NEWS ‎‎‎Mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress party- MCP Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wavomeleza kugonya...
24/09/2025



‎BREAKING NEWS


‎Mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress party- MCP Dr. Lazarus McCarthy Chakwera wavomeleza kugonya pachisankho cha Lachiwiri pa 16 September ndipo wafunira mafuno abwino tsogoleri wa Democratic Progressive Party-DPP Professor Arthur Peter Mutharika pakupambana kwake.

‎Dr Chakwera anane izi pomwe akuyankhula ku ntundu wa aMalawi pa wailesi ya MBC.

‎Bungwe loyendetsa chisankho dziko lino la MEC likuyembekezeka kuwulutsa zotsatira zayemwe wapambana pachisankho masana alero nthawi ya 2 koloko kuchokera ku BICC komwe kuli national tally centre.


‎(Wolemba Thom Kamanga)

 ‎‎Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission-MEC layamba layimitsa kae msonkhano wake wowulutsa yemwe w...
23/09/2025



‎Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission-MEC layamba layimitsa kae msonkhano wake wowulutsa yemwe wapambana pachisankho cha mtsogoleri kufikira Lachitatu 2 koloko masana.

‎Ganizoli ladza pamene m'tsogoleri wa Malawi Congress party- MCP Dr. Lazarus McCarthy Chakwera pamodzi ndi chipani chake anatenga chiletso choyimitsa kuwulutsa zotsatira zachisankho.

‎Komabe bwalo lamilandu lakana pepholi ndipo lawunikira chipani cha MCP kuti pakhale kuwunikiranso malamulo akayendetsedwe ka chisankho ndi bungwe la MEC ndipo n'tchito yowulutsa zotsatira ipitilirebe.

‎Madzulo ano bungwe la MEC limayenera kuwulutsa zotsatira zachisankho cha m'tsogoleri za maboma 12 otsala komaso kuwulutsa m'tsogoleri yemwe wapambana.

‎(Wolemba Thom Kamanga)

 ‎ ‎‎Mtsogoleri wa Democratic Progressive Party-DPP Professor Arthur Peter Mutharika ndiye akutsogolabe pachisankho cha ...
22/09/2025




‎Mtsogoleri wa Democratic Progressive Party-DPP Professor Arthur Peter Mutharika ndiye akutsogolabe pachisankho cha Lachiwiri pa 16 September ndi mavoti 2,022,879 pamene a Dr Lazarus McCarthy Chakwera achipani cha Malawi Congress-MCP akubwera pachiwiri ndi mavoti 722,494 kutengela pa maboma 24 omwe bungwe lachisankho la MEC la tsimikizira.

‎Izi zikudza pamene nkulu wa MEC Justice Annabel Mtalimanja watsimikizira zotsatira za maboma 11 pansonkhano wake lero ku Lilongwe.

‎Justice Mtalimanja wapitilira kulangiza azipani kuti zisiye kuchita zionetsero kapena kuvina vina munsewu chifukwa choti kutero sikungakakamize bungweri kutulutsa zotsatira zachisankho.

‎Maboma awulutsidwa lero ndi Thyolo, Dowa, Zomba, LiLongwe city, Balaka, Mzimba, Blantyre City, Nsanje Machinga komaso Nkhota-Kota.

‎(Wolemba Thom Kamanga)

‎ ‎ ‎‎Bungwe la Civil Society Elections Integrity Forum lapempha zipani kuti zipewe mkangano komanso kusangalala maka mu...
22/09/2025




‎Bungwe la Civil Society Elections Integrity Forum lapempha zipani kuti zipewe mkangano komanso kusangalala maka munthawi iyi pomwe bungwe la MEC silinawulesi owina pachisankhochi.

‎Iwo alankhula izi leroli pomwe anali ndi msonkhano wa atolankhani ku Lifestyle Hotel, Lilongwe womwe cholinga chake chinali kulimbikitsa zipani komaso ozitsatira awo kulimbikitsa bata.

‎Izi zikutsatiranso pamene otsatira chipani cha Malawi Congress-MCP chinachititsa zionetsero zowonetsa zowonetsa kusakondwa ndi momwe chisankho yandera.


‎(Wolemba Mercy Viola Mhango)

 Yemwe anaimira ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko mchipani cha Malawi Congress Party Engineer Vitumbiko Mumba wane...
21/09/2025



Yemwe anaimira ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko mchipani cha Malawi Congress Party Engineer Vitumbiko Mumba wanena motsindika kuti chipani chao chapambana zisankho za chaka chino. A Mumba anena izi pomwe anachititsa msonkhano wa atolankhani ku hotela ya Sunbird Capital mu mzinda wa Lilongwe pamoddzi ndi akuluakulu a MCP monga a Jessie Kabwira, Ken Msonda, Vera Kamtukure mwa ena.

Mkuyankhula kwao a Mumba ati chipani cha DPP chawabera ma voti ndipo ali ndi ma umboni ogwirika omwe ena anawapeza ku chilumba cha Likoma, Thyolo ndi boma la Dedza.

Engineer Mumba watinso MCP yapenzanso kuti ma "monitor" a DPP amasintha zotsatira za chisankho ku Mangochi masongola ndipo iwo apereka kale madando awo ku bungwe la Malawi Electural Commission, MEC.

Mwa zolakwika zina zomwe Chipani cha MCP chapeza nthawi ya zisankhoyi wachiwiri kwa mtsogoleri wa Kongeresiyu watinso oyang'anira chisankho awo ankathamangitsidwa nthawi yowerengera mavoti ndi anthu a DPP komanso wati ndiodabwa ndi kuchuluka kwa mavoti owonongeka (void votes) chaka chino zomwe wati sizinachitikeko ndikale lonse.

(Wolemba Jamie Michael)

 ‎ ‎‎Yemwe amapikisana nawo pachisankho cha Utsogoleri wadziko ngati oyima payekha  Abel James Chingulo wavomereza kugon...
20/09/2025




‎Yemwe amapikisana nawo pachisankho cha Utsogoleri wadziko ngati oyima payekha Abel James Chingulo wavomereza kugonja pachisankho pamene bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) ikupitilira ndi n'tchito yowerengela zotsatira.

‎Pakuyakhula pa msonkhano wa wolemba nkhani lero ku Crown Hotel ku Lilongwe, a Chingulo ati ganizoli ladza kutsatira kuchepa kwa mavoti osatsimikiza apeza.

‎Iwo alimbikitsanso a Malawi kuti asunge bata ndi mtendele pamene tonse tikudikirabe bungwe la MEC kuwulutsa zotsatira zovomelezeka.

‎Achingulo apitilira podzipeleka kugwira n'tchito ndi yense atenge boma pakutha kwa chisankhochi kuti adzathe kugwirtsa n'tchito ukadawulo wawo pankhani za Ulimi ndi zamalonda kuti miyoya ya aMalawi idzapite patsogolo.

‎Pakadali pano enaso mwa atsogoleri avomeleza kugonja pa chisankhochi ndi monga a Phunziro Mvula, Smart Swira ndi a Frank Mwenifumbo.

‎(Wolemba Jamie Michael)

Address

Muwula Street 10
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when GBS Your Family TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share