24/04/2026
Mighty Wanderers FC yapeza jersey sponsorship partner watsopano ya ndalama yokwana 200 million kwa chaka kuchokera ku Kingbossi yomwe ndi yogulitsa njinga zamoto. Komano zikuoneka kuti ma "replica" jersey ambiri a consignment ya season ino omwe akugulitsidwa ali dominated ndi 888 bets yomwe zikumveka kuti ubale ndi noma unatha. Practically zikuthauza kuti team idzivala Kingbossi ma sapota 888 bets . Zaka ziwili zapitazo ma sapota amavala ma jersey osiyana ndi omwe ma player amavala yet pogulitsa ankati ndi ma "replica".
Ma "replica" a 888 anabwera ndi inprint yochoka ku factory and anali a season yomwe ino kusonyeza kuti sizinali zodzidzimukila. Kodi kwenikweni panavuta ndi pati kapena zimavuta pati?, Ndiye kuti 888 bets will get free advertising?, Komanso ndiye kuti aliyense obwera amafuna chizindikiro chake chidzikhala kutsogolo kwa jersey komanso large signage? Mosaphweketsa 200 mita, mwina ma team adzilola kit sponsorship ina idzipita ku training kit kapena pa arm.
Paja main sponsor wa league logo yake ikufunikanso pa front pompo π