Timveni Online

Timveni Online Timveni is a child and youth media organisation, which comprises of Radio, Television & Social Media.
(4)

Omenyera ufulu wa anthu, Billy Malata, walengeza kuti walowa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu, chomwe mtsogoleri wake ...
06/07/2025

Omenyera ufulu wa anthu, Billy Malata, walengeza kuti walowa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu, chomwe mtsogoleri wake ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Michael Usi.

Malata wati amakhulupirira kuika chitukuko patsogolo, ndale pambuyo.

Iye wati adzaimira chipanichi ngati khansala wadera la Kasemba kudera la phungu wakunyumba ya malamulo la M'buka ku Lilongwe.

Malata wati akufuna kutukula derali ngati anthu kumeneko adzamusankhe pa chisankho cha chapa 16 September chaka chino.

Wolemba: Johans Mumba

Mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights Education, Advice and Assistance (CHREAA) Victor Mhango, wati ndi okhumudwa k...
06/07/2025

Mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights Education, Advice and Assistance (CHREAA) Victor Mhango, wati ndi okhumudwa kuti pa m'ndandanda wa akaidi omwe akhululukidwa, palibe maina a kaidi omwe anasankhidwa kuti akachite maphunziro ku sukulu za ukachenjede.

Mhango, wati uku ndi kuphwanya ufulu wa akaidi maka pa nkhani za maphunziro.

Izi zikudza pamene m'tsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, wakhululukira akaidi 37, ngat mbali imodzi ya chikondwerero kuti dziko lino lakwanitsa zaka 61 likudzilamulira pa lokha.

Ena mwa akaidi omwe akhululukidwawa ndi omwe agwira ukaidi kwa theka la zaka zawo zomwe analamulidwa, omwe akudwala komanso achikulire.

Wolemba: Phillimon Backson

06/07/2025

Timveni Exclusive with Dyson Jangiya Mneneri wa chipani cha UDF.

06/07/2025

Timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya Flames yagonja 3-0 kudzera pamapeto ndi timu ya Botswana pamasewero okondwerera zaka 61 za ufulu odzilamulira.

Masewerowa analipo lero pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe.

Maxwell Paipi, MacDonald Lameck komanso Nickson Mwase anaphonya mapenote awo onse, pamene Thabo, Ronald komanso Mosha anagoletsa mapenote awo zomwe zapangitsa Botswana kukhala akatswiri a chikhochi.

Thabang Sesinyi anatsogoza alendowa mumphindi yoyamba ya chigawo chachiwiri, ndipo Olson Kanjira anabweza kutangotsala mphindi 12 kuti masewero afike kumapeto.

Wolemba: Richard Tiyesi

Timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya anyamata osapyola zaka 20 yafanana mphamvu ndi timu ya mpira wamiyendo ya dziko...
06/07/2025

Timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya anyamata osapyola zaka 20 yafanana mphamvu ndi timu ya mpira wamiyendo ya dziko la Angola pogoletsana chigoli chimodzi kwa chimodzi ku mpikisano wa Region 5 Youth Games.

Masewerowa analipo lero pa bwalo la Hage Geingob m'dziko la Namibia.

Mwisho Mhango anatsogoza anyamata a Millias Jegwe mumphindi 16, ndipo Clemente Vicente Goncalves anabweza mumphindi zoonjezera za chigawo choyamba.

Malawi ili mugulu A momwenso muli matimu a Namibia, Angola komanso Zimbabwe.

Masewero otsatira alipo lachiwiri likudzali pamene akumane ndi Namibia pa bwalo lomweli.

Wolemba: Richard Tiyesi

 President of Botswana, Duma Boko, has asked Malawians to promote and observe peace in the run-up to the September polls...
06/07/2025



President of Botswana, Duma Boko, has asked Malawians to promote and observe peace in the run-up to the September polls.

Boko, who was speaking on the sidelines of Malawi’s 61st Independence anniversary in Lilongwe, said peace is central to economic transformation.

He expressed optimism that Malawi can transform into a better nation in Africa.

Meanwhile, Boko has hailed the existing cordial relationship between Malawi and Botswana.

Reported by Johans Mumba

 Mtsogoleri wadziko lino, Lazarus Chakwera watsindika kuti pakhale kugwirana manja pomanga maziko olimba otukula dziko l...
06/07/2025



Mtsogoleri wadziko lino, Lazarus Chakwera watsindika kuti pakhale kugwirana manja pomanga maziko olimba otukula dziko lino.

Chakwera wati aliyense yemwe ali nzika ali ndi mbali yake yokwanitsa ntchitoyi kuphatikizapo kusamala katundu pamalo ogwira ntchito.

Mtsogoleri wadziko linoyu watsindikanso zakufunika kosunga chinkhalidwe.

Mwambo wa chaka chino okumbukira kuti dziko lino lakwanitsa zaka 61 liri pa ufulu odzilamulira, ukuchitika pamutu oti; "Kubwezeretsa maziko oonongeka ndikupititsa Malawi patsogolo."

Wolemba: Johans Mumba

06/07/2025



Wapampando wakomiti yanduna yomwe ikuyang'anira mwambo okumbukira kuti dziko lino lakwanitsa zaka 61 liri pa ufulu odzilamulira, Ezekiel Ching'oma, watsindika zakufunika kokhala ndi mwambowu polimbikitsa umodzi m'dziko muno.

Ching'oma wati umodzi komanso kukonda dziko ndi kofunikira pa chitukuko.

Wolemba: Johans Mumba

 Anthu ena omwe abwera ku bwalo la zamawesero la Bingu ku Lilongwe adandaula kuti akulephera kuonera bwino zomwe zikuchi...
06/07/2025



Anthu ena omwe abwera ku bwalo la zamawesero la Bingu ku Lilongwe adandaula kuti akulephera kuonera bwino zomwe zikuchitika, kamba kakusagwira ntchito kwa kanema yaikulu yomwe anthu amatha kuonera zochitika ali mubwaloli.

Khebu Likangala yemwe amachokera kwa Njewa ku Lilongwe wati pamayenera kuti zochitikazi zikuonetsedwanso pa kanemayu.

"Zimakhala bwino kuti kanemayu izionetsa zomwe zikuchitika kuno kuti tizitha kuona bwino zochitika," watero Likangala.

Timveni yamvetsedwa kuti kanemayu anaonongeka ndipo kuti amangoonetsa mbali imodzi.

Akulu-akulu oyang'anira bwaloli sanayankhulepo kaye pankhaniyi.

Wolemba: Johans Mumba

06/07/2025

Apolisi akusaka-saka anthu omwe apha bambo wina wa zaka 65, Jester Salamba, m'dera la Masambanjati, m'boma la Thyolo.

Mneneri wa polisi ya Masambanjati, Amos Banda, wati thupi la bamboyu linapezeka lachisanu madzulo, m'mbali mwa mtsinje wa Michizu lili ndi mabala m'mutu komanso m'miyendo.

Banda wati malemuwa anatsanzika m'mawa wa tsikulo kuti akupita ku munda, koma sanabwelerenso kufikira nthawi yomwe thupi lawo linapezeka madzulo ake.

Achipatala atayeza thupi la malemuwa anapeza kuti anafa kamba kotaya magazi ambiri kutsatira kukhapidwa.

Wolemba: Susanna Nkhoma

Mtsogoleri wa dziko la Botswana, Duma Boko komanso mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, afika pa bwalo la zamawes...
06/07/2025

Mtsogoleri wa dziko la Botswana, Duma Boko komanso mtsogoleri wa dziko lino, Lazarus Chakwera, afika pa bwalo la zamawesero la Bingu mzinda wa Lilongwe.

Awiriwa akutsogolera mwambo okumbukira kuti dziko lino lakwanitsa zaka 61 liri pa ufulu odzilamulira.

Zina mwa zochitika ndikuphatikizapo maimbidwe komanso pelete wa asilikali ankhondo.

Masanawa pakhale masewero ampira wamiyendo pakati pa matimu a Malawi ndi Botswana.

Wolemba: Johans Mumba

Happy Independence Day!
06/07/2025

Happy Independence Day!

Address

712
Lilongwe
265

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Timveni Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Timveni Online:

Share