
15/07/2025
Apolisi ku Nkhata-bay amanga bambo wina wa zaka 39 pomuganizira kuti wagona ndi msungwana wa zaka 15 yemwe ali ndi vuto la mu ubongo.
Malinga ndi apolisi m'bomali, bamboyu wapanga izi pa malo ena ogona alendo.
Iwo ati msungwanayu adapita pa malowa chifukwa amagwira ganyu wotunga madzi.
Mkuluyu atawona msungwanayu nkumukokera mchipinda chomwe iye adali ndi kugona naye.
Pofuna kuti asakaulure kwa anthu, mkosanayu adapereka 800 kwacha kwa mwanayu.
Koma mwanayu adakauza mayi ake, womwe adakanena ku polisi ndipo apolisi agwira mkuluyu akufuna adzithawira ku Mozambique.