30/07/2025
Mwadzuka bwanji okondedwa omvera?
Inu ndi mdalitso ku TWR,ndichifukwa chake timakunyadilani ndi program ya Chimwemwenmmawa from 06:10 mpaka 07:00 mmawa(Mon- fri)
Lero tikambilane nkhani ya anthu amene safuna kukhazikika pamalo antchito,business even pa banja kumene ena sakhalitsa😂
Kuyamba ntchito osatha chaka unva akuti asiya.
Komatu mawu a Mulungu pa Miyambo 22 v 29 amati " Kodi ukumuona munthu wa luso pa ntchito yake?
Iye adzatumikira mafumu sadzatumikira anthu wamba."Koma anthu tikulephera kupezeka pamaso pa mafumu ndiko kupeza zabwino chifukwa chosakhazikika,kudekha pamalo antchito.
Kudekha pamalo kumapangitsabkuti otilemba ntchito atikhulupilire.Pa malo pamakhala zinthunzina zimene zimachitika ife osadziwa kumakambilana za promotion yako we ukuganiza zosiya ntchito.
Know that trust is earned and its a long term work setting.
Ena tasemphana ndi mwayi chifukwa chakusakhazikika pa malo.Abwana kuti afike pokusiila ma Key akuchipinda,ai galimoto mukhoza kumakagona nayo kwanu it means akukhulupilira.
Koma izi sizingachitike kwa kanthawi kochepa.
Kumadekha😂
Ndemanga zanu nzotani?
fans