02/08/2025
.
Pomwe kumacha loweruka, anthu ena omwe akuti adamanga mipanda yawo yanjerwa mosatsatira malamulo ku area 3 adzuka atabalalika kamba koti khosolo ya mzindawu yagwetsa mipandayo.
Mipanda yomwe ayigwetsayi ati adayimanga pamwamba pamalo omwe ma payipi a madzi a bungwe Lilongwe water board adadutsa, zomwe ati ndi chiopsyezo ku miyoyo ndi katundu wa anthu komaso kuphwanya malamulo a malo adziko lino.
Malinga ndi nduna ya malo m'dziko muno a Deus Gumba boma likuonetsetsa kuti aliyese m'dziko muno akutsatira malamulo pochita ntchito za zomangamanga ndipo ati iwo akukhulupilira kuti aliyese ayamba kutsatiradi malamulowa.
Sabata ziwiri zapitazi unduna wa malo wagwetsa zomangamanga zingapo zomwe ati sizinatsatire ndondomeko ndi malamulo a malo adziko pozikhazikitsa, ndipo nduna mu undunawu yafusa aliyese kuti azitsatira ndondomeko komaso kufusa nzeru kwa adindo asadayambitse chitukuko chirichonse cha zomangamanga.