
27/08/2025
Khonsolo yamzinda wa Lilongwe yati tsopano iyamba kulimbikitsa lamulo lokakamiza eni galimoto zonse zonyamula katundu okwana kapena kuposera matani khumi ndi asanu (15), kutenga chilolezo cholowera mu mzipata za m'zindawu kuchokera ku khonsoloyi asanalowe mu mzindawu nthawi ya usiku.
Mumkalata yomwe khosoloyi yatulutsa, izitu ndi molingana ndi mphamvu zomwe khonsoloyi ili nazo zapansewu zomwe cholinga chake ndikupereka chitetezo mu mzindawu, kwa oyendetsa galimoto.
Eni galimotozi ati akuyenera kumatenga chilolezocho masana kapena chakumadzulo ku ofesi zakhonsoloyi a Chidzanja nthawi yoti alowe mu mzindawu isanakwane.
Malinga ndi mkulu wa khonsoloyi Dr. Macloud Kadam'manja Galimoto zonse zomwe zichepsye izi azizilanda ndi kuzitsekera, komanso eni ake azipereka chindapusa mogwirizana ndi malamulo.