29/10/2025
Bwalo la Principal Resident Magistrate ku Lilongwe lati lipeleka chigamulo chake mawa, papempho la belo lomwe anthu 9 omwe akuwaganizila kuti adamenya, kukhapa ndikuchita chipongwe Sylvester Namiwa apeleka.
Anthu asanu ndi anayiwa akana milandu yonse isanu ndi umodzi (6).
Mmodzi mwaoimila milandu mbali yaboma Senior supretendent Moja Phiri wati iwo atsutsa pempho labeloli chifukwa anthuwa akatuluka akhonza kuthawa mwazina, pomwe yemwe akuimila oganizilidwawa Chrispine Mndala wati oganizilidwawa sangathawe chifukwa ali ndi mawanja, komanso amachita malonda awo mu Lilongwe mommuno mwazina.
Wolemba Robert Edward.