02/01/2026
Nyumba zofalitsa uthenga zomwe zinatsekedwa kapena kulandidwa zitupa m’zaka khumi zapitazi zapatsidwa chiyembekezo chatsopano, kutsatira chisankho chatsopano cha bungwe loyang’anira zoulutsira uthenga m’dziko muno, MACRA.
Bungweli latsegula mwayi kwa makampani okhudzidwa kuti alembenso mapepala ofotokoza chidwi chawo, ngati akufuna kuti zitupa zawo zibwezeretsedwe. Malinga ndi kalata yolembedwa ndi mkulu ogwirizira wa MACRA, Mayamiko Nkoloma, makampaniwo apatsidwa masiku 21 kuti apereke mafunso awo.
MACRA yati mwayiwu ukupereka mpata kwa nyumba zofalitsa uthenga zomwe zinalandidwa zilolezo zawo m’zaka khumi zapitazi, kuti ziwunikenso mmene zingabwererenso pa mphepo ya zoulutsira uthenga m’dziko muno.
Zina mwa nyumba zofalitsa uthenga zomwe zingapindule ndi chisankhochi ndi mawayilesi a kanema ndi mawayilesi omvera monga Beyond FM, Rainbow TV, Joy Radio, Ufulu FM, Galaxy FM ndi Sapitwa FM, omwe anali atatsekedwa m’zaka zapitazi.
Wolemba: Gift Tembo