21/08/2026
BREAKING NEWS
MA NEEDY STUDENTS FEES AYIMVERA FUNGO CHAKA CHINO KU MA UNIVERSITY.
Ophunzira a sukulu zaukachenjede ochokera m'makomo osaukitsitsa pafupifupi 14,000 akuyenera kudzipezera okha komwe apeze school fees chifukwa boma lawataya paliponse.
Izi ndi malingama ndi bungwe lopeleka ngongole kwa ophunzirawa la Higher Education Student's Loans and Grants Board(HESLGB) lomwe lalengeza lero m'boma la Salima kuti latenga ophunzira okwana 33,254 okha basi mwa ophunzira 46,386 omwe analembera bungweli kupempha ngongole yama phunziro.
Izi zikuchitika boma litakweza school fees m'ma universities a boma ndi 100% kuchoka pa K650,000 kufika pa K1,300,000 pa chaka.
Iziso ndizosemphana ndi zomwe nduna ya zamaphunziro a Bright Msaka anauza mtundu wa a Malawi kuti asadandaule popeza needy student aliyese yemwe anapanga apply loan ku loans board atengedwa pofuna kuti asamve ululu wakukwezedwa kwa school fees.
BOLA CHAKWERA YEMWE UJA, A MALAWI PA 16 SEPTEMBER TINAYAMWA TONDE!!!