29/04/2026
Pali chiyembekezo choti chiwerengelo cha fodya yemwe akukanidwa pansika chitsika potsatira zokambirana zomwe bungwe lomwe limaona za ulimi wa fodya mdziko muno la To***co Commission (TC) likuchita ndi kampani zogula fodya komanso unduna wa zamalimidwe.
Malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa, mbali zitatuzi zikhala zikuunikira zomwe zikuchititsa kuti mlingo ochuluka wa fodya udzikanidwa pa nsika ndikupeza mayankho oti akomere mbali zonse.
Ma belo a fodya okwana 95 pa 100 aliwonse akumabwenzedwa pa nsika kamba ka zifukwa zosiyasiyana ndipo izi zakwiyitsa alimi omwe anaopsyeza kuti achita zionetsero kamba ka nkhaniyi. Masiku apitawa, bungweli linakumana ndi ogula komanso alimi a fodya komwe mwa zina anagwirizana zoimitsa lingaliro lochita zionetserozi.
Bungwe la TC lati lidziwitsa alimi afodya za zotsatira za zokambiranazi mawa lachinayi pa 30 April.
Wolemba: Kenneth Luciano