Eye of an Eagle Malawi

Eye of an Eagle Malawi 0 881 673 119

Independent presidential hopeful, Thoko Banda, has described the 16 September elections as a great opportunity for Malaw...
02/09/2025

Independent presidential hopeful, Thoko Banda, has described the 16 September elections as a great opportunity for Malawians to choose whether to remain one of the poorest nations or to start growing economically.

Banda said both the current and past leadership have failed to eradicate poverty, instead enriching themselves without considering the welfare of poor Malawians.

Among other things, he said that once voted into power, he will ensure that 50 plus one percent of business opportunities will be reserved for Malawians.

Banda has therefore accused past administrations of failing to end hunger in the country.

“I don't understand why the government allows Malawians to be stricken by hunger when we have everything it takes to produce more maize. The problem of hunger in our country is man-made and people’s suffering is used for political gain.They cause hunger so that, when they give people food during campaign periods people must cheer them up. This will end once I am voted into power," he said.

Thoko Banda who is the son of the iconic politician, the late Aleke Banda, has therefore urged people to vote for an independent president, independent members of parliament, and ward councillors if Malawi is to develop.
#

Tsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera tsopano wayankha pempho la ophunzira za malamulo Ku sukulu ya ukache...
26/07/2025

Tsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera tsopano wayankha pempho la ophunzira za malamulo Ku sukulu ya ukachenjede ya Blantyre International University, Happy Makhalira komanso magulu ena okhuzidwa omwe analembera Kalata mtsogoleriyu k*ti ayitanitse aphungu k*t akonze gawo 74 mu malamulo achisankho.

Malinga ndi chikalata chomwe Makhalira analembera mtsogoleriyu masiku apitawo, lamuloli ndilophwanya ufulu wa anthu ena oponya vote kuphatikizapo ophunzira msukulu za ukachenjede omwe panthawi yoponya vote azakhala asalikumadera omwe analembetsera mukaundula wa vote.

Muchikalata chochokera mu office ya mtsogoleriyu chomwe Eye of an Eagle yawona, chati President Chakwera tsopano waitanitsa aphunguwa pa 5 August k*ti akakambilane zokhuza malumulo achisankho.

Poyankhula ndi Happy Makhalira ophunzira malamulo Ku BIU wati ndiokondwa tsopano k*ti a Chakwera anva Kulira kwa anthu ochuluka.

"Ndine otsangalala kwambiri k*ti tsogoleri wadziko lino wagwiritsa ntchito mphanvu Zake zomwe zili mu gawo 67(4) yamalamulo akulu adziko lino poitananso aphunguwa k*ti akonze lamuloli. Zaonetseratu poyera k*ti tilindi president yemwe ndiokunva Komanso olemekeza ufulu wa anthu", watero Makhalira.

Gawo 74 mu malamulo achisankho limakakamiza aliyense Kuponya vote Kumalo omwe analembetsera.

Kupanda kulikonza lamuloli kukanakhuza ophunzira mtsukulu za ukachenjede, achitetezo, ogwira ntchito abungwe la MEC Komanso atolankhani omwe azagwire ntchito zawo Kutali ndikomwe analembetsera vote.
#

Ophunzira za Malamulo Ku sukulu ya ukachenjede ya Blantyre International University Happy Makhalira walembera Kalata ofe...
25/07/2025

Ophunzira za Malamulo Ku sukulu ya ukachenjede ya Blantyre International University Happy Makhalira walembera Kalata ofesi ya pulezidenti ndi nduna kupempha mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera k*ti ayitanitse mkumano wa aphungu akunyumba ya Malamulo mwansanga pofuna kukonza gawo 74 mumalamulo oyendetsera chisankho.

Iye wati lamulori liletsa anthu ena kuponya vote kuphatikizapo ophunzira m'sukulu za ukachenjede omwe analembetsera Ku madera akwawo ponena k*t panthawi yoponya vote azakhala ali kusukulu osati kwao.

Lamuloli likukakamiza aliyense Kuponya vote m'malo omwe analembetsera kapena k*tsamutsira mayina awo.

"Mwachisanzo ophunzira m'sukulu za ukachenjede omwe analembetsera m'makawo ngati ine, sindingakwanitse kuyenda mtunda wautali k*ti ndikaponye vote kwathu," watero Makhalira.

Muchikalatachi chomwe Eye of an Eagle yawona, Makhalira watinso lamuloli ndilophwanya ndime 40(3) Komanso 77(1) mumalamulo akulu adziko lino constitution.

"Pokhala mtsogoleri yemwe amalemekeza ufulu wa mzika zonse ndipo analumbira k*teteza constitution, ndikukhulupilira k*ti a president salora k*ti maufuluwa aphwanyidwe," chatero chikalatacho.

Masiku apitawo, wapampando wa bungwe loyendetsa zisankho mayi Anabel Mtalimanja anawuza olemba nkhani Ku Lilongwe k*ti lamuloli likhuza ngakhale ogwira ntchito pachisankhochi monga, adindo ochokera kubungwe la MEC, a chitetezo, atolankhani ndi ena, omwe panthawiyi sazakhala Kumadera omwe analembetsera mukaundula wa vote.

#

Mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive professor DPP,  Peter Mutharika wati akukhulupilira k*ti bata lipitilira...
25/07/2025

Mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive professor DPP, Peter Mutharika wati akukhulupilira k*ti bata lipitilira muchipanichi ngakhale pali akulu akulu ena sanakondwe ndikusankhidwa kwa a Jane Ansah kukhala wachiwiri wawo pachisankho chikubwerachi.

Iwo anena izi pomwe amapeleka zikalata ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC lero ku Lilongwe.

A Mutharika ati sizikanatheka kusankha aliyense muchipanichi kotero akuyenera kuvomeleza ndikugwira ntchito ndi mayi Ansah.

Iwo ati alindi chikhulupilira k*ti mayi Ansah awathandiza k*tukula dziko lino akapambana zisankho za pa 16 September chaka chino.

Anthu ochuluka ovala makaka achipani cha DPP Komanso zipani zina monga Alliance For Democracy AFORD, Liberation for Economic Freedom anakachitira umboni mwambowu Ku BICC.

The International Fellowship of Pastors and Churches (IFPC) Malawi says preparations for a three day mega crusade schedu...
16/07/2025

The International Fellowship of Pastors and Churches (IFPC) Malawi says preparations for a three day mega crusade scheduled to take place from 1st to 3rd August are at an advanced stage.

Speaking to Eye of an Eagle Malawi, IFPC Malawi overseer Apostle James Nkhoma Labana said the crusade will take place at Balaka Secondary School grounds in Balaka District.

"Everything is going well and God continues to be faithful. We want to present the country's challenges to God so that He may heal our nation. We are going through hardships as a nation, and we want God's intervention. We will also pray for a peaceful election as we head towards the polls on 16th September," said Apostle Labana.

He has therefore appealed to well-wishers to support them financially to help cover some of the expenses.

Men of God from Ghana, Uganda, Zimbabwe, Zambia and South Africa are expected to grace the event.

#

Ngati njira imodzi yolimbikitsa umodzi pakati pazipani zandale bungwe la atolankhani la Blantyre Press Club yapempha aku...
26/12/2024

Ngati njira imodzi yolimbikitsa umodzi pakati pazipani zandale bungwe la atolankhani la Blantyre Press Club yapempha akulu akulu azipani k*ti akhazikike pofotokoza mfundo zawo osati kunyozana pomwe dziko la Malawi likupita kuchisankho chaka chamawa.

Tsogoleri wabungweri Luke Chimwaza wanena izi pomwe akonza msonkhano waukulu wapachaka omwe uchitike pa 27 December2024 m'boma la Mulanje.

"Ife atolankhani pokhala kamwa ya a Malawi tilindi udindo obweletsa pamodzi andale kuwafotokozera k*ti a Malawi akufuna chitukuko osati kunyozana kotero akufunika azifotokoza m'mene azathetsere mavuto omwe anthu akukumana nawo osati kunyozana. Pa ichi tatiana azipani zosiyanasiyana kumsonkhanowu", atero a Chimwaza.

Mwambuwu ukuyembekezera kubweretsa pamodzi zipipani monga MCP, DPP, UDF, UTM, AFORD kungotchula zochepa chabe.

Mthumwi Kuchokera Ku MEC, NICE Trust Komanso Salima sugar zikhala nawonso pamsonkhanuwu.

Wolemba Happy Makhalira- Blantyre

16/10/2024

Zipani za Democratic progressive DPP, United Transformation Movement UTM ndi Alliance for Democracy AFORD ati mkulu wa bungwe loyendetsa chisankho la MEC a Anabel Mtalimanja atule pansi udindo ponena k*ti akukayikitsa ngati agwire ntchito yokomera mzika za dziko lino pachisankho chikubwera chaka cha mawa.

Zipanizi zanena izi ma nsonkhono wa olemba nkhani omwe ukuchitikira ku Lilongwe.

Mwa ena omwe ali pansonkhanowu ndi mlembi wankulu wa UTM Dr Patricia Kaliyati, wachiwiri kwa tsogoleri wa AFORD Timothy Mtambo mlembi wamkulu wa DPP a Peter Mukhitho, a Bright Msaka, Shadrake Namalomba ndi ena.

Zipanizi zati bungwe la MEC lapanga hayala kampane ya Smartmatics yoti izagwire ntchito powerengera mavoti ngakhale k*ti kampaneyi ilindimbiri yosokoneza zisankho m`mayiko ena.

Wolemba Happy Makhalira

  #Mtsogoleri wa chipani cha LEF wapeleka asiku 14 kwa mtsogoleri wadziko lino Dr Lazurus Chakwera k*ti akhazikitse kafu...
12/10/2024

#

Mtsogoleri wa chipani cha LEF wapeleka asiku 14 kwa mtsogoleri wadziko lino Dr Lazurus Chakwera k*ti akhazikitse kafukufuku ndikupeleka lipoti la ngozi yomwe inapha wachiwiri wakale wadziko lino malemu Dr Saulos Chilima.

Iwo ati ngati izi sizichitika mumasiku amenewo iwo pamodzi ndi chipani cha LEF apita ku nyumba ya malamulo kukatula nykhawa zawo.

Iwo ati ino sinthawi yopanga mantha ndipo a Malawi akuyenera kudzuka ndikususana ndikupondelezedwa.

Iwo ati yakwana nthawi tsopano k*ti ndale za m`dziko muno zisinthe ndikuyamba kukomera mzika.

Wolemba Happy Makhalira

Mtsogoleri wa chipani cha LEF Dr David Mbewe tsopano ayamba kulankhula kuchikhamu cha anthu chomwe chafika pa bwalo la N...
12/10/2024

Mtsogoleri wa chipani cha LEF Dr David Mbewe tsopano ayamba kulankhula kuchikhamu cha anthu chomwe chafika pa bwalo la Nyambadwe primary School komwe chipanichi chikuchititsa msonkhano.

Uwu ndi msonkhano oyamba wachipanichi kuchokera pomwe chinalembetsedwa mu January Chaka Chino .

Wolemba Happy Makhalira _Blantyre

# #

Mtsogoleri wachipani cha Liberation for Economic Freedom Dr David Mbewe ndi mayi akunyumba mama Linda Mbewe afika pa bwa...
12/10/2024

Mtsogoleri wachipani cha Liberation for Economic Freedom Dr David Mbewe ndi mayi akunyumba mama Linda Mbewe afika pa bwalo la Nyambadwe primary School pomwe chipanichi chikuchititsa msonkhano.

Pabwaloli pafika anthu ochuluka omwe akufuna kunva zomwe Dr Mbewe akufuna kuwayankhula.

Wolemba Happy Makhalira_Blantyre
#

Woyimira anthu pa milandu Alexious Kamangira wakana kupepesa oweluza milandu Ku high court Ken Manda omwe amafuna Kuti a...
11/10/2024

Woyimira anthu pa milandu Alexious Kamangira wakana kupepesa oweluza milandu Ku high court Ken Manda omwe amafuna Kuti a Kamangira awapepese powaipisira mbiri.

A Ken Manda anafunsa a Kamangira Kuti awapepese ndi k250,000,000 komanso alembe uthenga owapepesa pa samba la Facebook ndipo a Kamangira atsindike Kuti zomwe akhala akulemba zokhuza a Manda ndizaboza.

Lawyer Alexious Kamangira wakhala akulemba Kuti judge Ken Manda ndiwakatangale ndipo amalandira ziphuphu Kuti azigamula milandu mokomera ena.

Koma poyankha pa pempho la a Manda lofuna kupepesedwa, layer Kamangira wati akasume ndipo iye sapepesa.

"Malinga ndikalata yofuna kupepesedwa yomwe munalemba m'malo mwa a Ken T Manda, chonde kasumeni", chatero chikalata chomwe a Kamangira alembera lawyer yemwe akuimira a Manda, Michael Goba Chipeta

Pakadalipano a Chipeta atenga chileso choketsa a Kamangira kulemba chilichonse chokhuza a Manda kufikira nkhaniyi itanvedwa ndi abwalo.

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lero wafika mu mzinda wa Blantyre pomwe akuyembekezeraka k*tsogolera masewer...
11/10/2024

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera lero wafika mu mzinda wa Blantyre pomwe akuyembekezeraka k*tsogolera masewero a golf loweluka ku country club ku Limbe mu mzindawu.

akuwoneka mwa mphanvu ndi thanzi Dr Chakwera atera pa bwalo landenge la chileka chakum`mawaku pomwe analandilidwa ndi akulu akulu aboma komanso aku chipani cha Malawi Congress.

masewero a golf wa cholinga chake ndik*tolera ndalama yothandizira ophunzira osowa m`sukulu za ukachenjede komanso k*thandizira anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe freddy.

#

Address

Chimwankhunda
Mount Pleasant

Telephone

+265881673119

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Eye of an Eagle Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share