27/05/2026
A polisi ku Lilongwe amanga anthu awiri omwe amadziwika kuti ndi mbava zotheratu chifukwa chopezeka ali ndi mfuti yokhala ndi zipolopolo zinayi popanda chilolezo ku Bwalolanjovu nthawi ya nkhomaliro Lachiwiri lapitali.
Anthu omwe amangidwawo ndi Steven Kanongola Kambwiri wa zaka 54 komanso Phillip Lazaro wa zaka 51, pomwe munthu wachitatu yemwe akungodziwika ndi dzina loti Jack Semu Kapilikitsa anathawa ndi galimoto ya mtundu wa Suzuki Swift.
Mneneri wa polisi ku Lilongwe Inspector Hastings Chigalu wati apolisi omwe amazungulira mu mzinda pofuna kukhwimitsa chitetezo adayimitsa galimoto yomwe anthuwo amagwiritsa ntchito ndipo atafufuza anapeza mfuti yodzaza ndi zipolopolo zinayi.
Wofalitsa nkhani za polisiyu wati Kambwiri ndi Kapilikitsa anali pa belo ya khoti pa mlandu wakuba ndi kuvulaza nzika ya ku India mu mwezi wa February chaka chino ku Area 9 mu mzinda wa Lilongwe pamene munthuyo ankachokera ku bizinesi zake.
Kambwiri omwe amachokera ku Dedza komanso Lazaro omwe amachokera ku Ntcheu akuyembekezeka kukaonekera ku khoti posachedwa kukayankha mlandu wopezeka ndi mfuti popanda chilolezo.
Wolemba: Damiano Fredson Kalajira