01/11/2025
Apolisi ku Blantyre amanga bambo wina pomuganizira mlandu wokuba ponamiza anthu kuti amagulitsa mbuzi.
Wachiwiri kwa m'neneri wa Polisi ya Blantyre Doris Mwitha wauza Mzati kuti oganiziridwayu ndi Raphael Saliva wa zaka 45 ndipo amachokera m'mudzi mwa Ngowi m'boma la Chikwawa.
Mwitha wati apolisi amanga mkuluyu lachisanu pa 31 October, ku Chikwawa komwe amabisala.
"tapeza kuti a Saliva akhala akuuza anthu kuti amagulitsa mbuzi ndipo ofuna azilipira kudzera pa lamya kuti awapititsire katunduyu, koma ofuna katundu wawo akatumiza ndalama iwo amadzimitsa lamya zawo", Mwitha watero.
Padakali pano m'neneriyu wati mlanduwu uli m'manja mwa apolisi owona milandu ya ndalama ndipo oganiziridwayu akaonekera ku bwalo lamilandu posachedwapa.
Chithunzi:Oganiziridwayu komanso Doris Mwitha yemwe ndi m'neneri wa apolisi.
Wolemba-Evance Rhonex Matola-Blantyre.