18/10/2025
MAINA ATHU NDI OMWE AMALEMBEDWA KUMWAMBA OSATI A MPINGO
Luka 10:2,20 Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzicuruka, koma anchito acepa; potero pemphani Mwini dzinthu, k*ti akankhe anchito kuk*tuta kwace. Koma musakondwera nako k*ti mizimu idakugonjerani, *koma kondwerani k*ti maina anu alembedwa m'Mwamba.*
Hallelujah 🙏 🙏 🔥
Eklesia wa Mulungu kuli ziphunzitso zonyoza mipingo ina k*t ngati timapemphera mpingo umenewo sitikapulumuka ndipo amatha kumapereka mavesi ngati zoona koma k*t muwafunse k*t ndi malemba ati amene amanena choncho sangakuuzeni k*tanthauza k*t chiphunzitso chawo chilibe umboni mmau a Mulungu ndipo mavesi omwe amapereka ndi osiyana ndi zinene amanena choncho mau a Mulungu ak*t tidzikondwera k*t maina athu alembedwa kumwamba kapena kunena k*t kumwamba munthu sadzaitanidwa ndi dzina la mpingo umene amapemphera koma lake iyeyo ndi ntchito zake ndi zimene ziti zidzamuchitire umboni choncho anthu atha kunyoza maina a mipingo ina koma sizik*tanthauza k*t mu mpingo umene amapemphera iwowo onse akapulumuka ayi opulumuka ndi amene maina awo alembedwa mu buku la moyo alembedwa kumwamba ndi ntchito zawo zabwino choncho ino ndi nthawi yolembetsa maina mu buku la Ambuye Yesu Khristu polapa machimo ndi k*tsikimizadi mtima kusiya zoipa mu dzina la Ambuye Yesu Khristu.
Apostle FM on 🎤🎙️