15/08/2026
MUKALOTA IZI NDIE KUTI MWANYAMULA ZA PAMWAMBA
AMOSI 3:7
By:Prophet Oswald Chizala
15 August, 2026
1.KULOTA UKUYENDETSA GALIMOTO
➡️Munthu woti m'moyo weniweniwu sukwanitsa kuyendetsa galimoto koma M'maloto nkumayendetsa galimoto bwino bwino osaphwanyitsa.
➡️Zimatanthaudza kuti mwa iwe muli utsogoleri womwe udzauyendetsa bwino bwino kwambiri.
➡️Pena zimatanthaudza kuti tsogolo lako liyenda bwino kwambiri.
2.KULOTA UKUPASIDWA NDODO
➡️Zimatanthaudza kuti ndiwe Munthu wa ulamuliro Mwachidule ukhala ndi udindo waukuru pa company, ufumu, utumiki komaso ku mabungwe ndi ku ndale.
➡️Maudindo ake ndi monga VP, president, Senior Chief ndi zina zotero.
3.KULOTA ULI NDI ANTHU APAMWAMBA.
➡️Zimatanthaudza chisomo cha kulumikidzika ndi anthu a pamwamba kwambiri.
➡️Pena zimatanthaudza kuti chomwe chiri mwa anthuwo chirinso mwa iwe.
4.KULOTA UKUPASIDWA MA KEY
➡️Zimatanthaudza kuti wanyamula family yakwanu, wanyamula mtundu wa kwanu, uli ndi ulamuliro pa zachuma koma zinthu zina zofunikira.
➡️Ukwaniritsa zinthu zambiri zikuluzikulu zomwe anthu ambiri maka azibale akukanika kuzikwaniritsa.
OFUNA THANDIDZO NDILANKHULENI PA NUMBER IYI
WHATSAP ONLY NO CALLS
(+265) 992 275 595
HALLELUJAH