
07/09/2025
TAPHUNZIRANI KUWERENGA MAU AMULUNGU NDIKUWACHITA.
Odala iye amene awerenga ndi iwo akumva mau achinenero nasunga zolembedwa momwemo pakuti nthawi yayandikira Chivumbulutso 1:3.
Mau AMulungu ndi moyo ukawadziwa sunganamizidwe tikuyenera kumawerenga mau ndikuwachita tsiku ndi tsiku .
Munthu amene amawerenga mau AMulungu ndikuwachita amakhala munthu amene moyo wa uzimu umakula.
Choyamba mukafuna Kuwerenga mau a Mulungu mupemphere kuti Mulungu akutsogolereni ndi mphamvu ya Mzimu oyera.mukayamba Kuwerenga musanapemphere sumumvesesa bwino.
Lapani Machimo mulandire chisomo cha Ambuye wathu Yesu khristu ndi mphamvu ya Mzimu oyera.
Mtendere wa Ambuye wathu Yesu khristu ukhale Nanu.
Follow BIBLE STUDY