
04/06/2025
Zikomo kwambiri kwa onse omwe anatenga nawo gawo kufalitsa mauthenga. Katundu yemwe anabwedwa wapezeka.
Apolisi yapa Game Stores Complex ku Lilongwe amanga a Shadreck Folly azaka 27 kamba kopezeka ndi zipangizo zamu studio yojambulira zinthuzi zomwe zinabedwa ku Mzuzu pa 31 May, 2025.
Malingana ndi mneneri wa polisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu, lero m'mawa oganizilidwayu anapita pa Game kusakasaka ojambula zithuzi, kukatsatsa katundu obedwayo.
A Chigalu koma ati munthu oganizilidwayu sanadziwe kuti anthu omwe anawafikirawo, anali akudziwa kale za katundu yemwe anabedwa ku Xian Creative Photo Studio ku Mzuzu.
Ojambulawa akuti anatsina khutu apolisi omwe anabwera kudzamanga oganizilidwayu. A Chigalu ati munthuyi atamufunsa mafunso wawulula kuti anagwilizana ndi alonda kuti abe katunduyo, yemwe ndiwa 4 million Kwacha.
Pakadali pano, apolisi at atumiza oganizilidwayu ku Mzuzu komwe anapalamula mlandu. Shadreck Folly ndiwochoka mmudzi mwa a Kajawa mfumu yayikulu Kadewere m'boma la Chiradzulu.
(by InnocentKumchedwa-Lilongwe;06/04/25)