23/12/2025
Nthambi yowona za panseu ya Malawi road traffic and safety services yapempha oyendetsa njinga za moto komanso magalimoto mu boma la Nkhata-Bay kuti atsatile malamulo a panseu mu nyengo ya zisangalalo.
Malingana ndi mkulu owona za mayendedwe a panseu ku nthambiyi, Clement Chipande, anthu ambiri amayendetsa njinga zamoto komanso magalimoto ataledzera munyengo ya zisangalalo zomwe zimapangitsa kuti ngozi za panseu zizichuluka.
Kamanga wapempha oyenda panseu kuti atsatile malamulo onse a panseu kuti ngozi za panseu zichepe.
Naye Khansala wa Chintheche ward, Moses Salem Kamanga, wapempha oyendetsa njinga mu boma la Nkhatabay kuti akhale osamala akamayenda panseu.
Malingana ndi nthambiyi, oyendetsa njinga pafupifupi 146 ndiomwe amwalira mu dziko lino kuchokela mu mwezi wa January kufika December chaka chino kamba ka ngozi za panseu.
Wolemba: Clive Mwafulirwa-Nkhatabay