12/06/2026
Mexico yayamba ndikupambana masewera ake oyamba mu 2026 FIFA World Cup pamene yatubula South Africa ndi zigoli ziwiri kwa duuu (2-0) pamasewero otsegulira mpikisanowu usiku wadzulo Lachinayi.
Julián Quiñones (9’) komanso Raul Jimenez (67’) ndi omwe anakhoma misomali pa Bafana Bafana kuti igonje 2 kwa chilowere pa masewero ochititsa jegunjewa.
Kupatula zigoi, Masewerowa kunaliso ma Red Card ochuluka kuposa zigoli, Sphephelo Sithole (49’) ndi Themba Zwane (79’) a South Africa komanso César Montes wa Mexico anapatsidwa ziphasozi.
Masewerowa anawoneledwa ndi anthu pafupifupi 1.1 Billion padziko lonse lapansi.