01/09/2026
A polisi m'boma la Nkhotakota amanga bambo Richard Lazarus wazaka 52 yemwe akuganizilidwa kuti anachita mchitidwe ogonana ndi mwana wake omupeza wazaka 14.
Mneneri wa polisi ya bomali Sergeant Chisomo Chuma wati bambowa anachita izi usiku omwe akazi awo anali atapita kumaliro.
"Bambowa analowa kuchipinda chomwe mwanayo amagona limodzi azibale ake, ndikuchita zosaweruzikazo. Mayi ake atabwera m'mawa, mwanayo anaulula zomwe zinachitika ndipo mayiwa atamva izi, anakatula nkhaniyi ku polisi ya Benga," watero Chuma.
Atatengeledwa kuchipatala cha Benga, azaumoyo anatsimikiza kuti mwanayo anachitilidwadi nkhanza yogonedwa.
Bambowa omwe ndi a m'mudzi mwa Bonga, Senior Chief Mwadzama m'boma lomweli akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwa.