
19/01/2024
ππ APHA ANA AKE KAMBA KOFUNA KUBISA UHULE WAKE
Bambo wina amene amagwira ntchito ku MRA anali pa night shift koma nkati mwa usiku anadwala, ndipo anapita pa clinic ya pafupi komwe anakalandira chithandizo. Usiku omwewo anabwelera kunyumba kwake, apa mpomwe anadabwa kuona galimoto la chilendo liri ku mpanda kwake. Atafufuza anazindikira k*ti mnyumbamo mwalowa mwamuna wina kuzathira batire π. Atalowa anawapeza awiriwo ali yedee, mchikondi cha n'nanu. Apa mpomwe analamula mkaziyo k*ti achoke mnyumba mwakemo, koma mkaziyo anachondelera k*ti kwada sangathe kuyenda ndiusiku koma alawilire mmawa. Mwamunayo mwa umunthu anamsiya mkazi wakeyo agone koma kuchipinda cha ana. Mkati mwa usiku mkazi anaganiza zofafaniza mwamuna wakeyo ( asakhalenso ndi moyo) poganizira za chitonzo angazakhale nacho akachoka pakhomopo.
Anakalowa mgalaja ndik*tengamo mafuta a petrol ndi kuyatsira nyumba ,bambo ndi ana ali mmwemo. Ana afera mmwemo kupulumukako bambo yekha amene ali muululu oopsa. Pakali pano mkaziyo ali mmanja mwa police ku Lilongwe .
FOLLOW OUR PAGE