
09/08/2025
Nsanje, Malawi — Pulogalamu ya Nyafisi Irrigation Scheme yomwe ili kwa Group Village Head Anne Petro, Mfumu Mbenje m’boma la Nsanje, yasanduka chithunzithunzi cha chiyembekezo kwa alimi, ikuwonetsa mmene ntchito za ulimi wothilira pogwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa zikhoza kusintha miyoyo ya anthu kumudzi komanso kulimbikitsa ulimi wothandiza chaka chonse.
Kuchokera ku Mavuto Kupita ku Chiyembekezo: Alimi Afotokoza Zomwe Akukumana Nazo
Kwa zaka zambiri, alimi ang’onoang’ono m’madera amenewa akumanapo ndi kusowa kwa mvula yokwanira, zokolola zochepa komanso ndalama zochepa. Lero, chifukwa cha dongosolo la solar-powered irrigation, alimi akhoza kulima ndi kukolola masamba chaka chonse komanso kupeza ndalama zokwanira.
“Tsopano ndimalipira ndalama za sukulu za ana anga, ndimagula sopo ndi chakudya,” watero Ruth Elias, m’modzi mwa amayi omwe akupindula ndi polojekitiyi. Iye akufuna kupititsa patsogolo nkhani zachuma pochita ulimi wa mbuzi.
Jambo Simon, mlimi wachinyamata, anenanso kuti pulogalamuyi ikulimbikitsa achinyamata ndi akulu mofanana. “Ife achinyamata tikutenga nawo mbali zonse, tili ofunitsitsa. Timagwira ntchito limodzi ndi akulu athu kuti pulogalamuyi ipitirire komanso tikhale ndi tsogolo labwino,” adatero Simon.
Zotsatira Zake Zapindulira Alimi ochuluka
Paul Mafambisa, wapampando wa Nyafisi Irrigation Scheme, anauza Gaka online kuti polojekitiyi yasintha kwambiri miyoyo ya alimi, ndipo tsopano amatha kukwaniritsa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku komanso kupanga mapulani a nthawi yayitali.
“Kusiyana kuli poyera. Mabanja athu amakhala bwino, amadya bwino komanso tili ndi chiyembekezo,” adatero Mafambisa.
Chofunika kwambiri, zabwino zomwe zikubwera ndi polojekitiyi sizimangokhudza alimi omwe ali m’pulogalamuyi.
Mlangizi wazaulimi ku Magoti EPA, Collins Walasi wati ngakhale anthu a m’madera ozungulira akugula masamba pa mtengo wotsika. Alimi sakukoloranso mbewu kamodzi pachaka, ena akukolora mpaka katatu chaka chimodzi.
“Izi ndi zomwe Malawi imafunikira,” adatero Walasi. “Zikugwirizana bwino ndi zolinga za Malawi Vision 2063, makamaka pa chakudya chokwanira komanso kusintha moyo wa anthu kumudzi.”
Thandizo la Othandizira Latsegulira Njira Yachitukuko Chokhazikika
Yoyambitsidwa mu 2023, Nyafisi Irrigation Scheme inathadizidwa ndi bungwe la Foundation for Active Civic Education (FACE), ndi thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la ALL WE CAN, la ku UK. Thandizo la alawo la solar irrigation system lalimbikitsa zokolola komanso lapatsa anthu m’mudzi zida zokhazikika za chitukuko komanso kupeza chuma mosalekeza.
Kusanthula: Pulogalamu Yoyenera Kuyesedwa m’madera Ena a Kumudzi
Pulogalamu ya Nyafisi si nkhani yoti ingopezeka kuderai kokha ayi, ndi chitsanzo choyenera kuyesedwa m’madera ena ambiri a Malawi. Ikuwonetsa kuti ngati dziko likonzekera kugwiritsa ntchito mphamvu zochokera ku dzuwa (renewable energy) komanso kuthandiza anthu osauka, ulimi wa kudalira mvula ukhoza kusintha kukhala ulimi wothandiza nthawi zonse.
Funso lalikulu ndi kuti pulogalamuyi ingatengedwe bwanji ku madera ena kumene alimi ambiri akadadalira mvula. Mgwirizano wa boma, ma NGO, ndi mabungwe othandizira ndiwo ofunika kwambiri.
Pomaliza: Kuchokera pa Kudalira Kupita ku Kudziyimira
Nkhani ya Nyafisi ikutiuza kuti kusintha kwenikweni kumachitika ngati anthu apatsidwa zida, mphamvu komanso chithandizo choyenera. Pamene alimi akukolola zotsatira za ntchito yawo, uthenga ndi uwui: ulimi wothiriridwa ndi madzi si madzi okha — ndi ulemu, mwayi, ndi chiyembekezo.
Wolemba; Yohane Chipula