Pastor Nohitoh messages

Pastor Nohitoh  messages soul winning campaign

04/05/2023

The race, the fight and the warfare
In Hebrews 12:1-2 we read:

Hebrews 12:1-2
“Therefore we also, since we are surrounded by so great a cloud of witnesses, let us lay aside every weight, and the sin which so easily ensnares us, and let us run with patience the race that is set before us, looking unto Jesus, the author and finisher of ourfaith, who for the joy that was set before Him endured the cross, despising the shame, and has sat down at the right hand of the throne of God. For consider Him who endured such hostility from sinners against Himself, lest you become weary and discouraged in your souls.”

We are called in this passage to run with patience the race that is set before us, looking unto Jesus the author and the finisher of our faith. The passage presents our Christian walk, our Christian life, as a race that we need to run:

1) with patience, and

2) looking unto Jesus, who is the author and finisher of our faith.

Paul in another place, in Philippians this time, speaks again about the race. There we read:

Philippians 3:12-14
“Not that I have already attained, or am already perfected; but I press on, that I may lay hold of that for which Christ Jesus has also laid hold of me. Brethren, I do not count myself to have apprehended; but one thing I do, forgetting those things which are behind and reaching forward to those things which are ahead, I press toward the goal for the prize of the upward call of God in Christ Jesus.”

Paul didn’t count himself as already having attained the prize. Instead he was dismissing those things that were behind pressing toward the prize of the upward call of God in Christ Jesus. There was a goal to be attained, a prize to be received. Paul didn’t consider this prize as already received. Instead he focused his life to receive this prize. He was goal oriented with the goal being the upward call of God in Christ Jesus.

Paul speaks again about the race and the prize in I Corinthians 9:24-27. There we read:

I Corinthians 9:24

23/08/2022

SATANA APONYEDWA PANSI
Muli bwanji?
leroso muli ndi ine m'nbale wanu mwa ambuye
KING NOHITOH pamene tikupitilizabe kuwunikirana kuchokera ku chibvumbulutso
chibvumbulutso 12:7
"ndipo kunali nkhondo kumwamba . mikayele ndi angelo ake amenyana ndi chinjoka ndi angelo ake."
bible likutiuza kuti kunali nkhondo kumwamba ndipo kunali magulu awiri , Mikayele ndi angelo ake ndi chinjoka chomwe ndi satana ndi angelo akenso . ndipo tiuzane pano kuti Mikayele anali mbali ya MULUNGU komanso amakhala kumbali ya anthu oyera mtima pamene akufunika kulowelera zikavuta daniel 12:1 ndipo ndi ufulu wanu kuyitanisa army yakumwamba pamene nkhondo yakula .komatu pamapeto pa zonse tikumva kuti satana anagonja pa nkhondoyi ndipo anaponyedwa pansi chibvumbulutso 12:9. tidziwisane mikayeli anatchulidwa ka 5 mu bible komanso azatengapo mbali pakuuka kwa akufa 1 atesalonika 4:16. pa yuda 1:9 tikumva kuti mikayele ndi amene anamuzusa mose mmanda .
kodi satana anamulenga ndi ndani?
ezekiyeli 28:15
"unali wa ngwiro mu njira zako kuchokera tsiku lomwe unalengedwa kufikira uchimo utapezeka mwa iwe ''
tidziwe ichi satana anali mngelo wa bwino kwambiri asanachimwe , ndipo ankatchedwa kuti lucifer yesaya 14:12 ndipo anali amene amabweretsa kuwunika mchifukwa chake a satanic greating yawo amati "hail the light". ndipo amadza ngati kuwunika pamoyo wa munthu ali ndi maplan owononga komanso bible linatichenjeza kale pa mateyu 7:15 kuti tichenjere ndi aneneri onyenga omwe amabwera ngati nkhosa , mwanjira ina satana akhoza kukuonekera ndi maonekedwe au MULUNGU ndicholinga choti akunyengeni chifukwa mukhoza kumangoti ndi ambuye ndi ambuye pang'ono pang'ono akukuchotsan pachikhulupiliro.
kodi chinalakwika ndi chani mwa satana?
ezekiyeli 28:17
chifukwa chakukongola kwake satana anayamba kuzikweza MMALO mongothokoza ndi maonekedwe ake.ndi ambiri lero omwe anatayika chifukwa cha maonekedwe komanso zomwe Mulungu ANAWAPATSA , ena anawalenga okongola mmalo mongoyamika achitenga ngati chida choti akhalire ndi amuna ochuluka, ena anawapatsa chuma chochuluka pano amaona kuti apite kutchalichi amaziona zofoyira . samalani ndi zomwe MULUNGU anakupasani zisakupangiseni kukhala kutali ndi MULUNGU. tikuona apa satana akusintha kuchoka ku munthu yemwe amabweresa kuunika ndikukhala munthu amene akubwelesano mdima.
kodi zolinga zake zinali zotani pomwe amaukira Mulungu?
yesaya 14:13-14
'"pakuti unati mu mtima mwako , ndikwera kunka mmwamba , ndikakweza mpando wanga pamwamba pa nyenyezi za MULUNGUY. ndipo ndizakhala ngati wa m'mwambamwambayo."
satana ankafuna kukwera ndikuyika ufumu wake pa mwamba kuti ampambane MULUNGU ndikutenga mpando wa Mulungu.
kodi anawina nkhondoyo ndi ndani>?
chibvumbulutso 12:9
"satana .... amene ananyenga dziko lonse anaponyedwa pansi ndi angelo ake anaponyedwa pamodzi naye"
tikutha kuona kuti kuwukira kwa satana kunali kwakukulu moti anakwanisaso kukopa 3 quarters ya angelo kukhala ku mbali yake. apa pati pase picture kuti satana sabwera mophweka akafuna kukwaniritsa ma plan ake tangoganizani kumukopa mngelo sichibwana koma iye anakwanisa kutero.
kodi ndi angelo angati omwe anaponyedwa limodzi ndi satana?
chibvumbulutso 12:4
mukawerenga mumva kuti satana anakwanitsa kukopa 3 quarters ya angelo pa nthawiyo sitikudziwa kuti panthawi kunali angelo angati , ndiye kuti quarter yokha ndi yomwe MULUNGU anatsala nayo. mupeza alemba kuti nyenyezi ndiye tinanena kuti nyenyezi imayimilira angelo.
kodi nkhondoyi inakathera kuti?
chibvumbulutso 12:12
"tsoka mtunda ndi mnyanja popeza oyipayo wasikira komweko"
apa tikutha kuona kuti nkhondoyi siyinathe ayi yangosintha malo ,kuchoka ku mwamba kubwera pansi pano mchifukwa chake satana nthawi zonse amakhala busy kusakasaka ana a Mulungu oti alikhwile
kodi mchifukwa chani Mulungu sadamuonongeretu satana nthawi yomweyo?
mateyu 13:29-30
"zisiyeni tiligu ndi nansongole zikule limodzi "
Mulungu akanamuononga satana nthawi yomweyo bwenzi anthu mukukaikira kuti satana anali olakwa kapena ayi ndipo akanamuononga bwenzi tikuti Mulungu amafuna kufufuta umboni .koma nokha mwazionera kuti satana ndioyipadi , mchifukwa chake akungodikira nthawi yake yoikika kuti satana azaonongedwe.

kodi ma plan asatana ndi otani?
1 peter 5:8
"satana , amawula ngati mkango , kufunafuna munthu oti awononge"
chibvumbulutso 12:13
"pamene chinjokacho chinaona kuti chaponyedwa pa dziko lapansi , chinalimbana ndi mzimayiyo"
chibvumbulutso 16:14
"pali mizimu ya ziwanda yochita zodabwitsa"
chibvumbulutso 13:14
"ndipo anawanyenga iwo akukhala pa dziko kudzera mu zodzizwisazo zomwe anali nazo mphamvu yozichita"
2 akorinto 11:14
"palibe kudabwa; pakuti satana yemwe adzionesa ngati mngelo wa kuunika.

Plan ya satana ndikusakasaka munthu oti amuononge , akhoza kuchia zozizwitsa .kuzisintha yekha kuobneka ngati yankho pavuto la munthu . koma chili chimbalangondo choononga.
kodi tingamuzindikire bwanji satana?
yesaya 8:20
"ku lamulo ndi umboni, ngati angayankhule mosemphana ndi mawu awa mchifukwa choti mulibe kuunika mwa iwo."
ngati mupeze kuti wina akuphunzitsa zosiyana ndi mawu a MULUNGU komanso malamulo ake dziwani kuti mulibe kuunika mwa iwo ndipo ndi abodza ma plan ndioti aphe , kuba komanso kukuonongani.
ngati simunalandire yesu kukhala mbuye ndi mpulumusi wa moyo wanu ndi nthawi yoti mulape chifukwa bible limati aliyense aliyense amene akhulupilira kuti yesu ndi ambuye yemweyo adzapulumusidwa aroma 10:9 ,ngati mwakhulupilira kuti yesu alipodi ndipo akhoza kukupulumutsani lapani lero chifukwa mphoto ya uchimo ndi imfa aroma 6:23 koma amene akhulupilira mwa yesu akhala ndi moyo wosatha yohane 3:36 ,ndipo mukalapa ndikupemphani mukhale ndi nthawi yoti mubatizidwe machitidwe 2:38 chooond nthawi yatha .
panganiko share kwa amnzanu asinthike nawo uthengawu
0995926996 texts only kapena tumizani message ku page yathu kapena pangani add keyng nohitoh ngati mukufuna thandizo la uzimu
ambuye akudalitseni
please share.

21/08/2022

CHIBVUMBULUTSO PART 2 IJA NDI IMENEYI
muli bwanji?
lero muli ndi ineso mtumiki wanu KING NOHITOH tipitilize pomwe tinalekera
choyamba tidziwe kuti pali aneneri ena omweso analemba zokhuza chilombo amene tikuti ndi satana . daniel anachitchula chilombochi kuti nyanga yaing'ono (little horn pa chingerezi ) yohane anachitchula kuti okana kristu ("Anti Christ ) pamene paulo anachitchula kuti mwana osaweruzika komanso munthu wauchimo ("the son of perdition" and "the man of sin).
tiyeni tilowe deep muzimenezi kaye
kodi chilombo chaku chibvumbulutso ndikuti kwina komwe chikupezeka?
daniel 7:3
ndipo zilombo zinayi zazikulu zinatuluka mnyanga
daniel:7:23
chilombo chachinayi .....chizaononga dziko lapansi (shall devour the whole earth)
daniel 7:8
ndipo pakati pawo panatulukaso nyanga ina yaing'ono. pa nyanga iyi panali maso onga ngati a munthu .
tikaona chilombo ichi sichikusiyanaso ndi chilombo chomwe tinachipeza mu chibvumvulutso 13 , pa chibvumbulutso 13 chilombo chija chinatuluka pa nyanja ndipo ichiso chikutuluka m'nyanja koma chili ndi nyanga khumi ,ndipo chili ndi mphamvuso pa dziko lonse kuphatikiza apo chikusogozedwaso ndi munthu. ndipo nyanga yaing'onoyi itithandiza kuti tidziwe kuti fano la chilombo ndi chani? Mark of the Beast is.
kodi chilombo chija cha ku chibvumbulutso 13 chikufanana pati ndi nyanga yaing'ono ya ku daniel 7 ?
daniel 7:25
adzayankhula mawu amwano motsusana ndi wamwambamwamba..., azakhala mpaka utha kwa nthaawi, ndipo azazunza oyera mtima.
tikutha kuona kuti zomwe chilombo ichi chikuchita ndi ndendende zomwe chilombo chakuchibvumbulutso 12 chikuchita ,,,,taonani
chibvumbulutso 12:6
ndipo mzimayiyo anathawila ku chipululu komwe MULUNGU anamukonzeratu kuti akamudyese kumeneko masiku 1260 .
chibvumbulutso 12:14
mzimayiyo anapasidwa mapiko awiri ...kuti awulukire ku chipululu , kuti akakhaleko ku nthawi za nthawi.
nthawi (time)mu prophetic meaning imayilimira chaka. nthawi za nthawi imayimilira zaka ziwiri.kugawika kwa nthawi imayimilira half ya chaka onani daniel 4:16, 23, 32; 7:25) zaka 7 zinasanduka kukhala zaka 7 '' ndiyeno nthawi ndi nthawi zanthawi ndi kugawika kwa nthawi zimapanga zaka zitatu ndi half yachaka pamene masiku 1260 aja tinanena kuti tsiku limayimiliraso chaka ndiyekuti apo tili ndi zaka 1260 zomwe zikufanana ndi miyezi 42 ya ulosi ija.
kodi nanga nyanga yaing'ono ikukakamizaso kuti anthu alandire fano la chilombo?
daniel 7:25
ndipo azayesera kusintha nthawi ndi malamulo.
kunena za nthawi apapa yomwe ikukambidwa apapa pa Malamulo a MULUNGU aja ndi sabata ,mchifukwa chake ena sadziwa kuti sabata lenileni ndi liti , sunday kapena surturday ? chifukwa ayesera kale kusintha nthawi zomwe zikusokoneza anthu panopa, calender anayitsokoneza kalekale , ngakhale chaka chimayenera chikhale ndi masiku 360 komanso masiku 30 pa mwezi sizodabwisa kumaona mwezi ukufika pa 31 wina kumatha pa 28 iyi ndi tchito ya satana chifukwa anthu oti mukupembedza MULUNGU mmodzi sitimayera kumakangana za tsiku lopemphera. imeneyo ndi action yomwe chilombochi chaonesa .
kodi chilombo (papa ) asinthapo nthawi?
eya
chibvumbulutso 13:6
anatsegula kamwa lake nanena mosusana ndi MULUNGU.
ma papa akuroma anasintha sabata lomwe lili saturday kukhala sunday pa zifukwa zawo umboni? werengani buku lotchedwa the Convert's Catechism of Catholic Doctrine pa page 50 maonekedwe ake titha kutumiza pic ku inbox ndipo anthu analora kumalambira sunday ena chifukwa choopa kuphedwa chifukwa samanyengelera ayi olo pang'ono koma anayiwala kuti kuvomereza sunday akhala akuvomereza lamulo la CHILOMBO kusiya la MULUNGU. werenganiko commentyi("Protestants…accept Sunday rather than Saturday as the day for public worship after the Catholic Church made the change… But the Protestant mind does not seem to realize that in observing Sunday, they are accepting the authority of the spokesman for the Church, the pope." Our Sunday Visitor, February 5, 1950)
chifukwa chani anthu otsusa maganizowa amalambira sunday mmalo mwa saturday?
chibvumbulutso 13:3
dziko lonse linadabwa nacho chilombocho.
dziko lonse ndilozizwa ndi mmene anthufe tikuchisatitilira chilombo. mukawere buku lija mupeza ma details onse a momwe akutipotozela pa chilungamo.
kodi tingatani lamulo la munthu, kaya la mpingo likusemphana ndi laMULO la MULUNGU?
machitidwe 5:29
''bola kumvera MULUNGU kusiyana ndi munthu''
mark 7:7
amandilambira ine pachabe, kumaphunzitsa ziphunzitsa malamulo a wanthu.
kodi tizizadindidwadi 666 monga fano la chilombo pa mphumi kapena pa zanja pathu?
chibvumbulutso 13:16
"chipangisa onse kuti alandire fano lake pa zanja lawo lamanja kapena pa mphumi pawo"
deutronomo 6:6,8
ayi tisayembekezere kudindidwa pa mphumi kapena pa zanja zomwe aliyense sangalole paja tinanena kale kuti mphumi imayimilira maganizo a munthu ndi zokhumba za mtima wanu, pamene zanja zintchito zathu.
kodi fano la chilombo ndi chani ( papa )
chibvumbulutso 14:11-12
"ndipo sapuma usana ndi utsik amene alambira chilombo ndi fano lake , ndi aliyense amene alandira fanolo mu dzina lache . apa pali chifatso cha oyera mtima :apa pali iwo amene asunga malamulo a MULUNGU , ndi chikhulupiliro mwa yesu.

kuchokera pa verseyo tikutha kusiyanitsa pakati pa anthu oyera mtima ndi anthu omwe avomeleza fano la chilombo. oyera mtima amasunga malamulo a MULUNGU kuphatikizapo sabata komano iwo amene akulambira fano la chilombo tamva kuti sakupuma usana ndi utsiku .tinakamba kuti sabata limatanthauza kuti kupumira ntchito (rest from labour ),oyipa sakupuma or mpang'ono chifukwa sabata sakulisunga. tidziwe ichi kupemphera sunday ndiko fano la chilombo tamvaniko ka statement aka "Sunday is our mark of authority. The church is above the Bible and this transference of Sabbath observance is proof of that fact." The Catholic Record, London Ontario, Sept. 1, 1923"
pomaliza fano la chilombo ndinganene kuti ndikumvera papa pamene anasintha tsiku la sabata ndipamene akulamula zinthu zoipa iwe nkumavera.
kodi chilombo kapena papa ali ndi thandizo pamene akukakamiza kuti anthu alandire fano lake?
chibvumbulutso 13:11-12
ndipo ndinaona chilombo china chikutuluka pansi, chinali ndi nyanga ngati zankhosa ndipo chinalankhula ngati chilombo . ndipo chinachita mphamvu zonse za chilombo choyamba pamaso pake ,ndikupangisa iwo akukhala pa dziko ndi iwo akukhalapo kuti akalambire chilombo choyamba chija.
choyamba choyamba chija chinatuluka pa nyanja koma ichi chikutuluka pansi.tinaphunzisana kuti nyanja imataunthauza kuti malo kapena dera lomwe komwe kuli chiwerengero cha anthu chochuluka (chibvumbulutso 17:15) .ngati nyanja ikuyimilira chiwerengero chochuluka cha anthu , ndiye kuti pansi pakuyimilira dera lomwe muli anthu ochepa.chilombo chachiwiri , kapena dziko ili likutuluka pa dera lomwe muli chiwerengero cha anthu ochepa.. komanso tamva kuti akuyankhula ngati nkhosa mwanjira ina ali ndi machitidwe owoneka achi christu kapena akuyankhula ngati au Mulungu. bible likuti chinadzuka pamene bala lake laku imfa lidapola la chilombo choyamba chija mu 1798 werengani verse 10. kodi dziko liti la mphamvu lomwe linadzuka atatha 1798, kuchokera mu dera la chiwerengero chochepa ndipo amene analiyambitsa ndi anthu amachitidwe ngati achi khristu? apa mupeza kuti ndi united states of america USA.
koma bible likuti xhilombochi chinasiya kuyankhula ngati nkhosa ndikuyankhula ngati chilombo.
ndikupangisa anthu okhala pa dziko lapansi kukakamiza kuti akalambire chilombo. bible apa likungolosera kuti USA izasiya kumenyera ufulu zachipembezo ndi machitidwe achi khristu ndikuthandizira papa kukamiza anthu kusatira malamulo omwe azipanga , ngati national sunday lawn (lamulo lokakamiza anthu onse kumapemphera sunday) , dziko limodzi , ndalama imodzi, kukwatirana amuna kapena akazi okha okha.
kodi USA ukuchita chani pochithandiza chilombo choyamba chija (papa)
chibvumbulutso 13:14
"ndikuwanyenga iwo akukhala pa dziko lapansi .... nanena achipangire fano lake chilombocho."
USA ipanga fano la chilombo chomwe ndi papa (chithunzi cha papa) ndipo musaiwale kuti mfumu nebukadinezala nayeso anapanga fano lake kuti anthu azililambira lomwe shadreck , mishek ndi abidinego anakana kulilambira pokana kuphwanya lamulo la MULUNGU loti usalambire milungu ina koma ine ndekha. tikati tione amzathu achikalika anayamba kale kumulambira mkulu ameneyi papa ..ndiye kukakamiza zinthu zomwe tazitchula zija iwe ndikugonjera uzikhala waphwanya malamulo a MULUNGU.
KODI USA Ikukakamiza bwanji fano la chilombo?
chibvumbulutso 13:15
"ndipo anali ndi mphamvu zopereka moyo kwa fano la chilombocho , kuti chilombocho chikayankhule ndikupangisa kuti aliyense amene sakuchilambira aphedwe.
chibvumbulutso 13:16
ndipo chinapangitsa onse , wa mng'ono ngakhale wankulu, olemera ndi osauka , mfulu ndi akapolo , kuti alandire fano la chilombolo pa mphumi zawo ndi pa zanja lawo lamanzere
USA Izi thandizila chilombo poyankhula ndikupangisa kuti anthu alandire fano la chilombo , kodi USA izizayankhula motani? izizayankhula popanga malamulo omwe dziko lonse lizizsatira ndipo chizapangisa dziko lonse kulandira fano la chilombo. kodi tadziwa bwanji kuti ndi catholic ikuyambitsa izi? werengani ka statement aka “Of course the Catholic Church claims the change was her act…and the act is a mark of her ecclesiastical power and authority in religious matters.” Office of Cardinal Gibbons, through Chancellor C.F. Thomas,Nov 11, 1895.
kodi alipo amene walandira fano la chilombochi panopa?
chibvumbulutso 13:17
"kuti palibe munthu amene adzagule ngakhale kugulitsa pokhapokha akhale ndi fano la chilombo."
palibe amene analandira lembo la chilombochi panopa pokhapokha zinthu tachula zija zitayamba kukakamizidwa ..kuphatikizapo economic sanctions kwa iwo amene azakane kuvomereza izi ..( mwanjira ina kuchotsa thandizo ndi zina zonse zomwe ziko limadalira kuti liyende bwino zizachotsedwa zomwe zizayambitse mavuto maiko ndipo mokakamizika maiko onse azavomeleza izi kungosala kuti munthu akane payekha. .. choyamba azapanga zoti musazamagule ngakhale kugulitsa pokhapokha mukhale nalo fano lake chibvumbulutso 13:17 . pomaliza anthu azizaphedwa akakana kulandira onani verse 15. koma panopa palibe amene ali nalo fano ngakhale ena amanena kuti ukabayisa covid 19 walembedwa 666 , mwina jakisoniyo ali ndi mphamvu yochepesa chiwerengero kapena kukupangisa kuti usamaganize mwa umunthu ndikukuononga chikhulupiliro chako.
kodi kuyipa kolandira fano la chilomboko nkotani?
chibvumbulutso 14:9-10
"ngati wina alambira chilombocho ndikulandira fano lake pa mphumi pake kapena pa zanja lake ,yemweyo adzalawa mkwiyo wa MULUNGU."
Mulungu adzasanulira mkwiyo wake pa aliyense olandira fanolo. azalandira mikwiyo isanu ndi iwiri pa chibvumbulutso 6:2 yomwe tiyilongosole bwino mtsogolomu.
pangani chisankho chabwino panokha musafere makolo , banja ngakhale makolo.
pa chithunzicho imeneyo ndi khani yomwe tikambirane mtsogolomu
nambala yanga ndi 0995926996 text only kapena tumizani message ku pageyi
ndipo timatumiza ma message achilimbikitso mungopanga hi pa nambalayo
pangani share kwa amnzanu please please please amve nawo uthengawu.

22/04/2022

Send a message to learn more

01/04/2022
01/04/2022

CHIFUKWA CHANI MULUNGU SAKUDALITSANI?
1.pakuti inu si MULUNGU amene mukondwera nacho choipa : ngakhale choipa sichidzakhala nanu.opusa sadzayima pamaso panu : mudana ndi onse ochita tchito zoipa" masalimo 5:4-5
izi zikutionesera kuti MULUNGU samakondwera konse ndi munthu ochita zoipa ngakhale utamapemphera maka bwanji chifukwa iye akuti amadana ndi onse ochita ntchito za mu m'dima, ndipo akuti opusa sadzaima pamaso pake , ena tapempha madalitso zinthu zochuluka pamaso pa MULUNGU koma palibe chikusintha chifukwa choti opusa( ochimwa) aliyense amene achita ntchito za mu mdima ambuye samulola kuyima pamaso pake mmene likufotokozera verseyo , muyenera kusintha kaye inuyo kuti mulankhule, ndikupempha zomwe mufuna kwa MULUNGU.
2.koma ntchito zanu zoipa zakulekanitsani inu ndi MULUNGU wanu , ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti sangamve. yesaya 59:2 ..pena ukhoza kumati mwina MULUNGU sangayankhe osamangoti sachedwa safulumira muzifunse kaye kuti kodi palibe malire pakati pa inu ndi MULUNGU , mmene tikuonera apa zikuonesa kuti MULUNGU samva mapemphero amunthu ochimwa chifukwa mumakhala ngati muli maiko osiyana pakufunika china chake Chomwe kuli kulapa kuti Muyambeso kulumikizana ndi MULUNGU.
3.akazi a chigololo inu ,kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi, uli udani ndi MULUNGU? potero , iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani la MULUNGU." yakobo 4:4 , apa zikutiwonesta kuti ngati munthu ukhala bwenzi la dziko mwanjira ina ukondweretsa dziko ndiye kuti umakhala wadana ndi MULUNGU chifukwa amene akulamulira dziko lapansi panopa ndi satana, ndipo ntchito za dziko panopa ndi zonyasa zokhazokha, ndipereka chitsanzo , wa mowa , wa fodya , anthu awawa amaoneka kuti ali ndi amzawo ochuluka ndipo dziko siliwatsala kuli konse komwe apite ndipo ngakhale ali mulendo amapeza anthu ocheza nawo ochuluka chifukwa anapanga ubale ndi dziko chifukwa cha fodya komanso mowa , koma kumbali mukaonesesa MULUNGU sakondwera nawo wa mowa, sakondwera nawo wa fodya , zomwe zikutionesa kuti ngati uli bwenzi wa dziko , ntchito zako zikondweretsa dziko ndiwe mdani wa MULUNGU. nde mdalitso amapereka ndi MULUNGU ndipo munthu sungapereke mdalitso kwa mwana amene sapanga zofuna zako ngakhale muli inu, sinthani kaye ndikukonzaso ubale wanu ndi MULUGu kuti zanu ziyambe kuyenda bwino.
4. MKHALIDWE OCHOSA MIMBAWU UTHE PLZ MULUNGU SANGATIPASE DZIKO LA MTENDERE NDI IZI TIZINGODA MA PRESIDENT OLAKWA TILI IFE CHOONDE NDI UDINDO WANU SHARE AND LIKE

30/03/2022

MKAZI KOMANSO MAMUNA PAYEKHA,
mkuluyu mukumuona apayu anabadwa wa mkazi dzina lake thomas beatie koma patapita ka nthawi anayamba mchitidwe ogonana akazi okha okha zomwe zinampangitsa iye kuti akachotsetse mabere ( mawere ake ) her breasts ) kuti iyeo azioneka ngati mamuna pamene akugonana ndipo mukaonesesa muona kuti mbali mwa mawere akewo muona kuti ka operation kanayenda ndithu anapanga izi chifukwa choti kutenga pathupi zimakanika. komano izo padera mkazi mnzake amene amagonana nayeyu amakanikaso kutenga pa thupi kwa amuna ena pa chifukwa ichi anagwiritsa ntchito njira ija imagwiritsidwa ntchito kuti ng'ombe itenge bere , ( using a home insemination kit ) ndipo zinathekadi kukhala ndi pathupi> mmene mukuoneramo.............
komatu izi sizimukondweretsa MULUNGU ayi uku kumakhala ngati ukusutsana ndi chilengede cha MULUNGU, khalidwe logonana akazi kapena amuna okha okha ndi zina zomwe MULUNGU samazikonda .

28/03/2022

ANA OTAYIDWA.
mkuluyu amapita mu zipatala zomwe zamuyandikira kumakatenga matupi a ana omwe anachotsedwa ku chipatala ( mimba zochotsedwa )/aborted babies ) iye amatenga ndikukaika mmanda ponena kuti awa ndi anthu ngati ife tomwe osati zinyalala zoti ziotchedwe kapena kutayidwa. MMENE MUKUONERA PA CHITHUNZIPO.
chonde lekani kuchosa mimba mimba , ma doctor ntchito isakupangiseni kutaya chipulumutso chonde, atsikana chitsikana chisakuchimwiseni kuti muzisangalala wina wake akuufuna moyo choonde.
parliament inavomereza kuchotsa mimba koma MULUNGU amaletsa izi eksodo 20:13

ngati muli okhuzidwa tumizani uthengawu kwa amnzanu ndi magulu osiyanasiyana.
ambuye akudalitseni pomwe mukufalitsa uthengawu.

28/03/2022

MWANA WA MA WEEK 6-7 NDIYE MUMATI MIMBAYO NDIYAING'ONO SIMUNAPHE ETI? LAPANI MSANGA PLZ SHARE AND LIKE OUR PAGE KUTI ZISAMAKUPHONYENI ....................

26/03/2022

kodi munamvapo za new world order? izi ndi dzina za zomwe zili mu mfundo zawo
1.ndalama imodzi
2.dziko limodzi
3.mpingo umodzi
4.mtsogoleli mmodzi
5.kukwatirana amuna kapena akazi okhaokha.
6.alimbikitsa ma tattoo
7.aphunzitsa anthu kuima ma style olambira satana pamene akujambulitsa chithunzi , kaya ndi nyimbo ngakhale film kuti anthu akopele ndikuzisata zomwe za falikira kale.
8.apanga zovala zokhala ndi zizindikiro monga za njoka, ma dragon , akazizi ndi zina zoopsa zomwe ziomagwira ntchito ngati bluetooth yotumizira ziwanda
9.alimbikitsa anthu kuti azikonda mipikisanu ngati ya mpira zomwe MULUNGU amadana nazo.
10.alisintha bible ndipo likhala lokomera iwowo

NGATI MUMAPANGA IZI MULI KALE MU NEW WORLD ORDER
1.kuvala zazifupi
2.kuvala zovala zachimuna pomwe ndiwe mkazi/mamuna kuvala za chikazi
3.tsitsi logula ngati weave, mesh ,komanso kuluka tsitsi momwe mungafunire
4.anyamata kusunga tsitsi lambiri
5.kukhwefula,\
more to come .......................

24/03/2022

KODI MUKUDZIWA? bible limaletsa mamuna kuvala chovala cha mkazi ndipo mkazi kuvala chovala cha mamuna , ndipo limalesaso kudulira mutu wanu komanso ndevu pamene mwametesa? limalesaso ma tatoo komanso kudya magazi ( mwazi )anyama ( ena amati uwende) wa nyama mukudziwa kodi? werengani levitiko chapter cha 18 mpaka 24 . kuti mudziwe zambiri

Address

Phalombe

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Pastor Nohitoh messages posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Pastor Nohitoh messages:

Share

Category