05/09/2025
Bwalo la Second Grade Magistrate m'boma la Salima lagamula bambo wa zaka 20, Emmauel Sesiyo Bakali kukakhala kundende kwa miyezi 18 ndikukagwira ntchito ya kalavula gaga kamba kakuba katundu wandalama zokwana K1,187,000 kumalo ogona alendo a Mpatsa ku Senga Bay mbomali.
Malinga ndi mneneri wa polisi ya Salima, Rabecca Ndiwate, khothi, kudzera mwa oyimila boma, Sergeant Grant Chiwalo, linamvetsedwa kuti usiku wapa 13 March, 2025 Bakali yemwe adagwirako ntchito ku malowa, adaphwanya chipinda china chapa malowa ndikuba filiji, television, nthambo, generator, matilesi, decorder ya DSTV komanso zofunda.
Achiwalo anauzaso khothi kuti apolisi akwanitsa kubwezeretsa katundu yense ku Shapevale mboma la Ntcheu komwe Bakili amabisala.
Atakaonekera kubwalo la milandu, Bakali anapezeka olakwa pa mlanduwu ndipo anauza boma kuti libweretse mboni zinayi zomwe zimatsusana naye.
Boma linalamula kuti opalamuyu alandire chilango chokhwima chifukwa mlanduwu ndiwaukulu.
Ngakhale opalamulayu anapempha kuti amuganizire, second Grade Magistrate Agness Chirambo, anagwirizana ndi boma ndikumulamula kukakhala kundende kukakhala kundende kwa miyezi 18 ndikugwira ntchito yakalavula gaga.
Bakali amachokera m'mudzi mwa Maiwaza, Mfumu yaikulu Kachindamoto mboma la Dedza.
Wolemba Tiyamike Makanga