
26/06/2025
Khonsolo ya boma la Salima yati ndi yokonzeka kugwira ntchito limodzi ndi atenga mbali osiyanasiyana powonetsetsa kuti amayi omwe akutenga nawo gawo pa ndale ndi otetezeka ku nkhanza pamene dziko lino likukonzekela chisankho cha pa 16 September.
Mmodzi mwa akulu akulu ku nkhonsoloyi Chipiliro Janet Mtambalika ndiye wanena izi pa mkumano omwe unakozedwa ndi mabungwe a Oxfam ndi Warlec ndicholinga chodziwitsa anthu pa za ubwino otengapo gawo pa ntchito yoteteza amayi omwe akupikisana nawo mmadindo osiyana siyana pa ndale.
Malinga ndi Mtambalika nthambi yowona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pa khosoloyi yachilimika pophunzitsa anthu pa za ubwino olemekeza amayi pa ndale.
Pothilirapo ndemanga nkulu wa nthambi ya polisi boma la Salima Albert Nyongani wati mikumano yophunzitsa anthu ndi mafumu komanso ochita malonda ku madera iwathandizira kuchepetsa chiwerengero cha nkhanza pa ndale pofuna kudzakhala ndi chisankho cha bata ndi mtendere.
Mau awo senior Chief Karonga adayamikira mabungwe a Oxfam, Worlec ndi atenga mbali osiyanasiyana kamba ka mkumanowu ponena kuti upindulila amayi pa ndale.
Mkumanowu udabweletsa pamodzi atenga mbali osiyana siyana monga mafumu, apolisi, atsogoleri a zipani kungotchurapo ochepa.
(Angella Mwape-Salima)