27/11/2025
MOYO WA THEBA
Theba siyimafuna ma singles...
Kaya ndiwe wa mkazi kaya ndiwe wa mmuna koma ngati uli SINGLE theba singakukonde...
Vuto ukakhala single moyo wako umauyika pa chiophyezo....
Tiyeni tiyambe ndi azimuna...
Mamuna yemwe Ali single kuno,amakhala pachiophsyezo chachikulu zedi chifukwa amadzolowera kukhala yekha ndiye ma RESPONSIBILITIES ake monga bambo amayamba kuwathawa.
Komanso thupi likayamba kutentha ndi izi amangotenga nazo azimai akunozi monga Zima kaladi zogweruka mano zokonda Old Brown sherry kapena achina NONDUMISO awa azimai a aliyense yemwe Ali ndi ndalama ya mowa kwa nthawi imeneyoyo....
Tikakamba za atsikana,mmmhhh...
Atsikana ndiye chifukwa chofuna ntchito ,ndalama ya chakudya kapena ndalama ya RENT,aku SHOWEDWA nazo ndi amuna onvetsa chisoni ku theba kuno...
Maka Maka akafuna kupanga zitukuko ku Malawi ndiye eeehhh azimuna amachita kukhala nawo mbweeeee..
Wina wa rent wina wachipeleganyu wina wa ma groceries.....
Mkazi mmodzi koma amuna mbweeee
Kufuna kupanga chitukuko kumalawi.
Ndizija zitukuko zimatheka koma mwini wake osakagonamo kukangofikila kumwalira kuli kutenga zotenga tenga....
Ndiye kuno zimafunika ukangofika theba kaya ndiwe wa mkazi kaya ndiwe wa mamuna gwira ntchito pang'ono then itanitsa mkazi wako kapena mamuna wako...
Kumeneku ndiye kupewa zambiri....
Komabe KHUMBO LANGA ndiloti ngati SIMUDABWEREKO KU THEBA MUSADZABWERENSO...
Ili ndi khumbo langa nanunso muli nalo khumbo LANU....