
27/01/2024
🇲🇼NKHANI YA NKHONDO YOMWE IKUPITILILA KU UKRAINE
Maiko a Russia ndi Ukraine, Dzulo anagwilizana zochita Msintho kuti asinthane Asilikali a Maiko awiriwo omwe anagwidwa pa Nkhondo.
Ndipo Msinthowo umayenera kuchitika pa Malo ena otchedwa Kolotilovka, ku Malire a Maiko a Russia ndi Ukraine.
Koma Ndege ya Asiliakali a Dziko la Russia, a Nkhondo ya Mlenga Lenga, inanyamuka ku Khamba Lokhala Asilikali a Dzikolo, Lotchedwa Chkalovsky, kufupi ndi Mzinda wa Moscow, pa Ulendo opita ku Chigawo cha Belgorod, chomwe chinachita Malire ndi Dziko la Ukraine.
Ndipo Asilikali a Dziko la Ukraine, anaombera ndi kugwetsa pansi Ndegeyo ndi Mabomba atatu a mtundu otchedwa Mizailo, ochokera ku Zida za Nkhondo za Maiko a Germany ndi America, ponena kuti Ndegeyo inanyamura Mabomba a mtundu otchedwa S-300, ndicholinga choti akaphulitsidwe pa Nkhondo yomwe ikupitilira M'dzikolo.
Koma Dziko la Russia, Lati mu Ndegeyo munali Asilikali a Dziko la Ukraine okwana 65, omwe anali pa Ulendo opita ku Msintho, komanso munali Asilikali atatu(3) omwe amapelekeza Ndegeyo, komanso Anthu ena Asanu ndi M'modzi(6) ogwira ntchito mu Ndegeyo.
Ndipo Anthu onse pamodzi anakwana 74, omwe afera pa Malo pomwe Ndegeyo yagwera.
Ndegeyo yagwetsedwa pansi kufupi ndi Tauni yotchedwa Yablonovo, Mchigawo cha Belgorod.
Ndipo poyankhulapo pa Nkhaniyi, Bambo Mark Voyger, yemwe anakhalapo Mlangizi wa Dziko la America pa nkhani zokhudza Dziko la Russia, anati ndizokayikitsa kuti mu Ndegeyo munali Asilikali a Dziko la Ukraine omwe amapita ku Msintho.
Komanso Bambo Muksym Kolesnikov, yemwe anapulumukira Mkamwa mwa Mbuzi kudzera pa Msintho, wati Iye anali mu Gulu la Asilikali a Dziko la Ukraine okwana 50, pa ulendo opita ku Msintho, Ndipo iwo ankatetezedwa ndi Asilikali a Dziko la Russia, okwana 20, choncho ndi zamkutu ndi zopanda pake kuti Asilikali a Dziko la Ukraine 65, angapelekezedwe ndi Asilikali a Dziko la Russia atatu (3) pa Ulendo opita ku Msintho.
Komanso Bambo Dmitro Lubinets, yemwe ndi Mkulu wa Bungwe Lowona za Maufulu a Nzika za Dziko la Ukraine, wati Maina a Asilikali a Dzikolo, omwe Dziko la Russia Likunena kuti amapita ku Msintho, anapeledwa kale ku Dzikolo, pa Msintho omwe unachitika pa 3rd January.