
13/07/2025
Chiwerengero cha anthu omwe akufuna mpando wa Phungu dera la Neno East sopano chafika pa anthu 13 kusatira kulengeza kwa ntolankhani Luke Chimwanza kuti wakatenga zikalata zake ku bungwe la MEC ndipo apikitsana nao ngati phungu oima paekha.
A Chimwanza omwe ndi mtsogoleri wa a ntolankhani chigawo cha ku mwera-Blantyre press Club ndiye kuti akhala ntolankhani wachiwiri kuimira ku dera la Neno East pambuyo pa a Patrick Kamkwatira omwe nao anatula pansi ntchito ku wailesi ya Times.
A Chimwanza amachokera m'mudzi mwa Tchenga ku Matope
Dera la Neno East ndi latsopano ku Neno, ndipo likukuta dera lonse lomwe liri pansi pa mfumu yaikulu Symon komwe kuli madera a Zalewa, Lisungwi, Matope ndi Kasamba kungotchulapo ochepa chabe