08/04/2026
Nthawi ya holiday ndi nthawi yosangalatsa kwa ena… koma kwa ana ena osowa, ndi nthawi yovuta kwambiri. Ena mwa iwo alibe chakudya chokwanira, alibe zovala zoyenera, ndipo sakudziwa ngati akabwerera kusukulu adzakhala ndi zipangizo zofunika monga mabuku, ma uniform kapena ma shoes.
Lero tikuyitanani inu nonse okoma mtima ❤️ kuti tigwirane manja pothandiza ana awa. Tiyeni tigawane zomwe tili nazo—ngakhale zingakhale zochepa—chifukwa kwa iwo zingakhale kusintha kwakukulu pa moyo wawo. Chakudya chimodzi chomwe inu mungaone ngati chaching’ono, kwa iwo chimakhala moyo. Chovala chimodzi chomwe inu simukuchigwiritsa ntchito, kwa iwo chimakhala chitetezo ndi ulemu.
Cholinga chathu ndi chakuti ana awa akamabwerera kusukulu, asamavutike kapena kudziona otsika mtengo chifukwa chosowa zofunikira. Tifuna tiwathandize kuti akhale ndi chiyembekezo, chidaliro, ndi mtima wophunzira bwino.
👉 Tikulandira:
Zakudya (ufa, mpunga, shuga, ndi zina)
Zovala (za ana a mitundu yonse)
Zipangizo za sukulu (mabuku, mapensulo, ma school bags, ndi zina)
Together we can make a difference.
Osadikirira kukhala ndi zambiri kuti uthandize… chofunika ndi mtima wokoma.
📩 Lumikizanani nafe kuti mudziwe momwe mungaperekere chithandizo.
0899168944 / 0984889974
Little acts of kindness can create a big impact.