17/08/2026
Zatsimikizika k*ti a Mavuto Witness, omwe anagundidwa ndi sitima pa mlatho wa Suluzi m’boma la Machinga pafupifupi ola limodzi lapitalo, amwalira.
Malume a malemuwa, a Mustafa Wailesi, atsimikizira Zodiak Online za imfayi ndipo ati a Mavuto, omwe amachokera m'mudzi wa Chilonga,mfumu yaikulu Malemia m’boma la Zomba, anali ndi vuto lakumva.
Zodiak Online itafika pa Chipatala cha Machinga, inapeza galimoto ya chipatala ik*tsitsa thupi la malemuwa kuliika mnyumba yachisoni.
Ngoziyi ndi yachiwiri kuchitika m’boma la Machinga, k*tsatira imfa ya mayi wazaka 72 yemwe nayenso anagundidwa ndi sitima m'masiku apitawa.