12/05/2021
WANDITAISA NTHAWI
#£√£√£√£√£√£√£√£√£√
PART 3
"Ndikakumana naye ndimuuza zonse za kukhosi".
Umuuza ndani? Aisha anafunsa atatulukira pa malopo mosayembekezereka.
Mmmmm ujeni, wafikanso nthawi yanji komanso watenga makope, ukuphunzira kuti?
Manuel, ndakuziizimusatu komamso ukuyankha kwa mantha, anyway ndikupita Ku sukulu.
Inenso ndikupita komweko koma ndimafuna ndidusire kwanu ndikakuone ndiye pakuti takumana ndi bobo basi.
Onse ananyamukira limodzi ulendo wa Ku sukulu, paja ndiwe wa primary muzilimbikiratu kuti muzakhonze.
Aisha kuyankhura ndi Manuel, ndi momodi nanga iwe uli kalasi yanji?
Ndili form 1 , ndiyetu tionana chifukwa ine ndimadusira uku, Aisha atamuuza kuti akusiyana naye, Manuel kukamwa kunamuuma, kuti ayankhure amalephera.
" Manuel ndikuti tionana, bwanji sukuyankha? Aisha kufunsa modabwa.
Ndingakupereke ? " kundiperekera!!!!!! iwetu uli ndi mau, yankhura usamangike.
Chabwino Aisha, ndinakukonda utakhala nzanga tizichenza.
Manuel ati kumeneko kufunsira, inetu sindimachenza ndi anyamata ndiye pepa Manuel.
Kodi ndati kuchenza, ndinalakwisa ndikufuna ukhale chibwenzi changa ndizikuthandiza chimene ukusowa.
Aisha atamva kuti akumufuna chibwenzi anamuyangàna Manuel kwa chidwi kenako anafunsa; " wati chibwenzi? inetu Ndili pa sukulu ndiye zinthu ziwiri sindingakwanise ukanandiuza njira ina osati chibwenzi.
Mau a Aisha anamubalalisa, njira yanji ukunenayo, inetu sindikudziwa ukunenazo.
Mmmmm Manuel sukuziwa,,,,, unamvapo za PTM?
Ayi ndi chipani chanji?
Si chipani, iweyo upite kwathu ukawauze makolo anga kuti ukufuna ndikamaliza sukulu uzandikwatire, akandifunsa ndizakubvomera ndiye iwe uziphunzira Inenso ndikuphunzira, tikazamaliza tizakwatirane basi.
Ndiye ukandibvomera tizikumananso kumbali kumachenza?
Manuel anafunsa pofuna kudziwa, kumbali ayi koma pamaso pa makolo anga komanso sitimakhala kwa tokha kuopera kuganiza zona ngakhalenso poyenda sitingayende awiri opanda wina wa pambali.
Zimene anayankhura Aisha zinali zachilendo kwa iye komabe anabvomera kutero.
Chabwino ndakumva, ndibwera mawa ndikaweruka Ku sukulu.
Anasiyana aliyense kumapita Ku sukulu imene amaphunzira.
Manuel atafika anakumana ndi Christopher nayenso akufika kumene.
"Manuel ameneyo, anzathu ndiye mwauswa ulusi" Christopher kumuyamikira nzake.
Mmmm nzanga wa primary akuchepera, taona timabvalatu kabudura ndiye pamenepo tinganene kuti wauswa?
Komabe ukuoneka bwino, uniform ya sopano komanso nsapato chimodzimozi.
Man, ndinamukonzekera Aisha kuti akandione bho .
Christopher anadabwa za nkhani imene waiyamba Manuel.
Aisha ndiye ndani? Christopher anafunsa.
Wina wake wa form 1 ndipo wabvomera koma akuti ndikaonekere kwa makolo ake ndikawauze kuti ndikufuna ndizamukwatire tikazamaliza sukulu.
Wooow ndi zabho, ameneyo akuoneka kuti ali ndi sogolo, akufuna aphunzire.
Mau amene anayankhura Christopher anamudabwisa, iwe ukugwirizana naye, ndizingocheza naye opanda kupanga chilichonse?
Kupanga chani, zinazi osamathamangira sizimatha, muzapanga nsogolo man, oky ndiye mupita kwawo kapena ndipite ndine?
Manuel anadziwa kuti mkadzi uja anamuuza za nzeru , anabvomera kupitadi kwa Aisha.
Akuchenza nthawi yokalowa mkalasi inakwana, anaphunzira mpaka kuweruka.
Christopher anaiwara zoti anamuuza Lidia kuti akumane koma Lidia sanaiware ndipo atamuona akupita osalabadiranso za iye anamuthamangira kukamupeza.
Lidia ukupita kuti? Christopher anafunsa,
Usandiuze kuti waiwara zoti umandifuna kuti tionane!!!!!!
Ooooh sorry ndinaiwara , Manuel sogola ndikupeza kapena tionana mawa.
Manuel ananyamukadi kumapita.
"Christopher, sindichedwa mayi anga akufuna anditume Ku nsika umandifuniranji?"
Funso la Lidia analiyankha mwa chidure, ndikufuna iweyo ukhale chibwenzi changa.
Lidia anayamba kaye kunyadanyada posafuna kuzitchipisa kuyankha ngati sakufuna,"Mmmm ayi, komanso ndili naye wina ndiye kuti ndivomere pompano Mmmmm ndizobvutirapo.
Christopher atamva mmene anayankhira Lidia sanalimbane naye.
Oky basi ndapita.
Lidia anadabwa ndi mmene anayankhira Christopher chifukwa amayembekezera kuti azimuchonderera koma ayi ndithu, ananyamuka kumapita.
Usapite iwe!!!!!! nanga tathana!!
Sanayangànenso mmbuyo ndipo anayamba kumuthamangira Manuel.
Lidia anaima kwa ka nthawi posamvesa kenako ananyamuka kumapita koma ali okhumudwa kwambiri.
Tsiku losatira Manuel anapita kwawo kwa Aisha nthawi ya Ku masana, atafika anawapeza bamboo ndi mayi a Aisha akuchenza.
Anaodira ndipo anamuyankha, " bwerani pafupi takulandirani".
Atafika anamufunsa chimene wabwerera ndipo anayamba kulongosola;
Manuel: Ine ndabwerera mwana wanu Aisha, ndimafuna chitomero cha banja.
Bambo ake: Chitomero!!! Mmmmm mwana wathu ali pa sukulu tikudikira akakhonza bwino timutumize ku college.
Manuel : Musadandaure ine ndizamudikira mpaka amalize.
Bambo ake : Ndikuti ayi!! kapena ukufuna uchoke chothamanga?
Bambo a Aisha akwiya, kodi zitha bwanji?
Pangani share kuti ena awerenge nawo.
Makoment anu amandilimbikisa.