
04/05/2025
Tamvani izi!
Mu 1978, abambo awiri anagwira anthu 30 mokakamiza pa restaurant yotchedwa Melbourne ndipo chomwe ankafuna nchoti munthu wina yemwe anali ku ndende, Chopper Read atulutsidwe.
Zili mkati, mmodzi mwa awiriwo, Amos Atkinson, anaitana mayi ake ndipo pamenepo ndi pomwe zinthu zinasanduka sewero.
Mayi akewo atafika, anayenda mwachindunji kudutsa apolisi panja ndi kukamkhoma mwana wawoyo ndi ka chikwama kawo ka mmanja.
"Leka zako zopusazo!" Iwo anatelo kwa mwana wawoyo ndipo nthawi yomweyo iye anagonja nkutulutsa anthu onse.
Mayi si munthu wamba!
Tipangeni follow kuti muzidziwa zina zambiri zochititsa chidwi!