Chanco Community Radio 107.6 FM

Chanco Community Radio 107.6 FM Available for live streaming on multiple platforms online. Let Our Light Shine | Nyale Iwale.

Two-time winner of AEJ Green Media House of the Year (2017 & 2024) Catch us on 107.6 FM in Zomba, Machinga, Phalombe, Mulanje, Chiradzulu, and surrounding areas. Chanco Community Radio was established by the University of Malawi with funding from the Royal Norwegian Embassy through the Lake Chilwa Basin Climate Change Adaptation Program (LCBCCAP), which was ran by the Department of Forestry throug

h the Forestry Research Institute of Malawi (FRIM), WorldFish, and Leadership for Environment and Development (LEAD) South-Eastern Africa. Chanco Community Radio began broadcasting to the Lake Chilwa Basin and surrounding areas on 6th July, 2013 and was officially launched on Monday 22nd July, 2013 by the then Minister of Environment and Natural Resources, Halima Daudi and the then Norwegian Ambassador, Asbjorn Edihammer. Chanco Community Radio's broadcasts are mainly focused on environmental management and climate change adaptation. The radio also broadcasts content on education, development, good governance, health, and general entertainment.

Lamulungu pa 20 July 2025 kuli mkokemkoke ku Ntaja!
19/07/2025

Lamulungu pa 20 July 2025 kuli mkokemkoke ku Ntaja!


18/07/2025

Bungwe la Malawi National Examinations Board (MANEB) latulutsa zotsatira zamayeso a ophunzira a m'sukulu zosula aphunzitsi a ku pulaimale.

Malinga ndi chikalata chomwe MANEB yatulutsa, mwa ophunzira 7, 132 omwe analemba mayeso, 7, 095 ndi omwe akhonza kuimira ophunzira 99 pa 100 alionse.

Mwa ophunzira aakazi 3, 923 omwe analemba mayesowa, 3, 908 ndi omwe akhonza ndipo mwa ophunzira aamuna 3, 209 omwe analemba mayesowa, 3, 187 ndi omwe akhonza.

Chikalatachi chafotokozanso kuti sukulu zisanu zomwe zapambana kuposa zina ndi Maryam Girls, Phalombe TTC, St. Joseph TTC, Dowa TTC komanso Mzimba TTC.

(Wolemba: Christina Ndalowa)

18/07/2025

NYIMBO ZAM’KHONDE MWATHU TOP 20
Lachisanu pa 18 July 2025

1. Waza – Whisper Mw
2. Watanganidwa – Egiry Mtoliro
3. Ndi Iweyo – Hot Ice
4. Tisatenthe Nkhalango – Nicholas Kwajama
5. Aborted Daughter – TK Stah Maxma ft. Shanjuh
6. Ndimakukonda – Raffick Potani ft. Collins Bandawe
7. Ndamkonda – Lester Nkhoma
8. Mwayenera – Stegal Mw ft. Carsticks
9. Ndikupembedzani – St Francis Choir (Namisonga)
10. Malume – Freshan
11. Waza – Chipi Namwino
12. Sunawone – Omi
13. Sukumvetsa – Sting Lex ft. Heri Cee
14. Phone – Osper ft. Mature
15. Aleke – Pre Mafia
16. Awiriwiri – Ramzy Sparta
17. Ndapeza – Born Dee
18. Dzina Lake Lasowa – James Kajawo
19. Amangoyang’ana – Real Fradilla
20. Changachanga – Culture Kondamache

Mwayi kwa nonse omwe mukuimira pa chisankho chomwe chikudzachi kuti muyale mfundo zanu anthu azidziwe.
17/07/2025

Mwayi kwa nonse omwe mukuimira pa chisankho chomwe chikudzachi kuti muyale mfundo zanu anthu azidziwe.

Bungwe lopereka ngongole kwa ophunzira m'sukulu za ukachenjede m'dziko muno la Higher Education Students Loans and Grant...
16/07/2025

Bungwe lopereka ngongole kwa ophunzira m'sukulu za ukachenjede m'dziko muno la Higher Education Students Loans and Grants Board (HESLGB), lati pafupifupi ophunzira okwana 3,000 sanapereke zonse zowayenereza kutenga nawo ngongole yamaphunziro ku bungweli pa nthawi yomwe amalembera ngongoleyi.

Mkulu woona zofalitsa nkhani ku bungweli, Millie Kasunda, wati ophunzira ochuluka sanapereke chipaso chaunzika chawo, mboni komanso umboni wotsimikiza kuti apereka ndalama yokwana K10, 000 ku banki.

“Ophunzira ambiri sanawerenge malamulo omwe tinapereka kuti atsatire asanalembere ngongoleyi. Ambiri sanapereke zikalata zoyenera, ndiye akuyenera kuti akonze izi pasanadutse pa 18 July chaka chino," watero Kasunda.

Iye watinso ophunzira omwe analembera ngongoleyi akuyenera kutsimikiza ngati anaperekadi zonse zowayenereza kuti alandire nawo ngongoleyi kudzera ku sukulu zawo.

Bungweli laperekanso mwayi kwa ophunzira omwe sanapereke mapepala onse owayenereza kulandira nawo ngongole kuti atha kutero pakadali pano mpaka pa 18 July, 2025.

(Wolemba: Isabel Molande)

In a bid to promote the safety of children online, a Master of Arts in Media, Communication, and Development student at ...
15/07/2025

In a bid to promote the safety of children online, a Master of Arts in Media, Communication, and Development student at the University of Malawi (UNIMA) has developed an innovative WhatsApp chatbot named SafeChat Guardian. Click the link to read more.

In a bid to promote the safety of children online, a Master of Arts in Media, Communication, and Development student at the University of Malawi (UNIMA), Nathan Majawa, has developed an innovative WhatsApp chatbot named SafeChat Guardian. The project, which will run from 1st July to 31st July 2025,....

Nthambi yothandiza kuzimitsa moto mu mzinda wa Zomba yapulumutsa galimoto ina yomwe imakasiya katundu lero ku shop ya Az...
15/07/2025

Nthambi yothandiza kuzimitsa moto mu mzinda wa Zomba yapulumutsa galimoto ina yomwe imakasiya katundu lero ku shop ya Aziz mtauni ya Zomba yomwe inayamba kuyaka.

Anthu omwe anaona izi zikuchitika auza Chanco Community Radio kuti ataona kuti yayamba kuyaka anayamba kuithira dothi ndipo posakhalitsa galimoto yothandiza kuzitsa moto ku khonsolo ya mzindawu inafika pamalopo ndikuyamba kuthandiza kuzimitsa motowo.

Sabata yatha, anthu okwiya anabweza galimoto yothandiza kuzimitsa moto ya ku khonsoloyi itachedwa kufika pa malo pomwe minibus ina imkayaka pa msika wa Chinamwali ndipo potsatira izi, mneneri wa khonsolo ya mzinda wa Zomba Aubrey Moses analangiza anthu kuti azidziwitsa khonsoloyo mwachangu pakakhala ngozi ya moto.

(Wolemba: Tiamike Mao Njanji)

14/07/2025

Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi m’dziko muno, Noel Kayira, wati apolisi ndi okonzeka kupereka chitetezo mosakondera kwa aliyense amene akutenga nawo mbali pa chisankho cha pa 16 September 2025.

Polankhula pa mwambo okhazikitsa nyengo yokopa anthu omwe ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe, iye wati apolisi awonetsetsa kuti malamulo okhudzana ndi chisankho akutsatidwa mpaka pa nthawi yoponya voti.

“Tiyesetsa kupanga chothekera kuti kusakhale ziwawa ndipo aliyense okolozera kapena kuchita ziwawa amangidwe ndi kuzengedwa mlandu monga momwe malamulo akunenera,” watero Kayira.

Kayira wati anthu akuyeneranso kupewa mchitidwe wofalitsa mauthenga abodza makamaka kudzera m’masamba amchezo ponena kuti izi zili ndi kuthekera kodzetsa mpungwepungwe komanso kusokoneza kayendetsedwe ka zisankho.

Pakadali pano, bungwe la MEC lakhazikitsa buku la malamulo oyendetsera chisankho omwe zipani za ndale, omwe akupikisana ndi onse okhudzidwa akuyenera kutsatira pa nyengoyi.

(Wolemba: Jonas Kachikho)

14/07/2025

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lapempha atsogoleri azipani komanso onse omwe akupikisana nawo pa chisankho chomwe chichitike pa 16 September 2025 kuti apewe mchitidwe womwe ukhoza koyambitsa ziwawa pa nthawi yomwe akuchita misonkhano yokopa anthu kuti adzawavotere.

Mkulu woyang’anira chisankho ku bungwe la MEC, Andrew Mpesi, wapereka pempholi pa mwambo okhazikitsa nyengo yokopa anthu pokonzekera chisankhochi womwe ukuchitikira ku Bingu International Convention Centre mu mzinda wa Lilongwe mmawa uno.

Mpesi wati pakufunika mgwirizano wabwino pakati pa mbali zonse zokhudzidwa kuphatikizapo zipani zandale, atsogoleri a mipingo, magulu achitetezo komanso onse omwe akupikisana nawo kuti chisankhochi chidzayende bwino.

“Kupezeka kwanu ndi kutengapo mbali zikupereka uthenga kuti kukhala ndi chisankho chopambana si udindo wa MEC okha ayi. Aliyense akuyenera kutengapo mbali kuti kampeni ikhale ya bata ndi mtendere,” watero Mpesi.

Polankhula pamwambowu, wapampando wa bungwe la Centre for Multiparty Democracy, Ben Chakhame, wapempha onse omwe akupikisana nawo pachisankho chikudzachi kuti awonetsetse kuti akuwuza anthu mfundo zomwe akonza pofuna kupititsa dziko lino patsogolo.

“Tiyeni tipange kampeni yodziwitsa anthu mfundo zomwe tiri nazo osati kunyozana kuti chisankho chathu chidzakhale cha mtendere,” watero Chakhame.

(Wolemba: Jonas Kachikho)

13/07/2025

Timu ya Mighty Wanderers yagonjetsa Ekhaya FC ndi chigoli chimodzi kwa duu kudzera mu chigoli chomwe wagoletsa Gadi Chirwa m'chigawo chachiwiri.

Zateremu, Wanderers yakwera kufika pamwamba pa ligiyi ndi mapointi 29, kuchotsapo FCB Nyasa Big Bullets yomwe ili ndi mapointi 27 onse atasewera masewero khumi ndi amodzi.

Ku Rumphi, timu ya Moyale Barracks yalepherana ndi Silver Strikers pogoletsana chigoli chimodzichimodzi.

Moyale ndi yomwe inagoletsa chigoli koyamba kudzera mwa Raphael Phiri pa mphindi 31 m'chigawo choyamba.

Koma Zebron Kalima anagoletsa chigoli chomwe chafananitsa mphamvu matimuwa pa mphindi 73 m'chigawo chachiwiri.

Zateremu, Silver yakwera kufika pa nambala yachitatu mu ligi kuchotsapo Ekhaya ngakhale onse ali ndi mapointi 20 koma akusiyana zigoli poti Silver yagoletsa zochuluka.

Ku Mchinji pabwalo la Aubrey Dimba, Creck Sporting Club yagonjetsa Mzuzu City Hammers ndi chigoli chimodzi kwa duu chomwe chinagoletsedwa ndi Kondwani Chilembwe pa mphindi 61 m'chigawo chachiwiri.

Zateremu, Creck yakwera kufika pa nambala 8 pomwe Hammers yatsika kufika pa nambala 15 mu ligi yamatimu 16yi.

Ku Dedza, Premier Bet Dedza Dynamos yalepherana ndi Blue Eagles osagoletsana chigoli chilichonse komanso Karonga United yalepherana ndi Chitipa United posagoletsana chigoli.

(Wolemba: Raymond Siyaya Jnr.)

Masewero mu mpikisano wa TNM Super League akupitirira masanawa m'mabwalo osiyanasiyana.Timu ya Ekhaya FC yomwe ili pa na...
13/07/2025

Masewero mu mpikisano wa TNM Super League akupitirira masanawa m'mabwalo osiyanasiyana.

Timu ya Ekhaya FC yomwe ili pa nambala yachitatu mu ligi ili pakhomo kukumana ndi Mighty Wanderers yomwe ngati ipambane lero ikwera pamwamba kuchotsapo timu ya FCB Nyasa Big Bullets yomwe yagonja dzuro ndi timu ya Civil Service United.

Timu ya Silver Strikers, yomwe ikuteteza ligiyi, lero ili koyenda ku Rumphi komwe ikukumana ndi timu ya Moyale Barracks.

Pomwe timu ya Creck Sporting Club ili pabwalo la Aubrey Dimba kukumana ndi Mzuzu City Hammers.

Ku Dedza, Premier Bet Dedza Dynamos ili pakhomo pabwalo la Dedza kukumana ndi Blue Eagles.

Ndipo ku Karonga, Chitipa United yayenda kukumana ndi Karonga United yomwe ili pakhomo.

(Wolemba: Raymond Siyaya Jnr.)

12/07/2025

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets lero yagonja ndi timu ya Civil ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi mu mpikisano wa TNM Super League pa bwalo la Civil mu mzinda wa Lilongwe.

John Dambuleni ndi amene anagoletsa chigoli choyamba cha timu ya Civil pa mphindi 50 Bullets italephera kutchinjiriza kona.

Koma Bullets inabweza patangopita mphindi zisanu ndi ziwiri Civil kudzera mwa Ephraim Kumwenda yemwe anali atangolowa kumene.

Civil yagoletsa chigoli chopambanira kudzera mwa Moses Banda yemwe anasumba mpira Bullets italepheranso kutchinjiriza kona.

Zateremu, timu ya Mighty Wanderers ili ndi mwayi wotsogolera ligiyi ngati igonjetse Ekhaya FC pa bwalo la Kamuzu mawa lino pomwe ili yachiwiri ndi mapointi 26 ndipo Bullets ili ndi mapointi 27.

Ku Karonga, Kamuzu Barracks yagonjetsa Songwe Border FC ndi zigoli zitatu kwa chimodzi.

Samson Chiponda anagoletsa chigoli choyamba pa mphindi ziwiri komanso chachiwiri pa mphindi 44 mu chigawo choyamba.

Pamene Mwakikunga anagoletsera Songwe pa mphindi 63 kudzera pa penote m'chigawo chachiwiri ndipo Olson Kanjira ndi yemwe wagoletsa chigoli chachitatu cha Kamuzu Barracks pa mphindi 93.

Izi zikutanthauza kuti Songwe Border FC sinapambaneko masewero aliwonse chilowereni mu ligi yaikulu yadziko linoyi itasewera masewero khumi ndi awiri.

(Wolemba: Raymond Siyaya Jnr.)

Address

Zomba

Website

https://chancoradio.mw/

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Chanco Community Radio 107.6 FM posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Chanco Community Radio 107.6 FM:

Share

Category

Our Story

Chanco Community Radio is owned and run by Chancellor College, the main constituent college of the University of Malawi. The radio started broadcasting in on 6th July 2013 but was officially launched on 22nd July 2013 by the then Minister of Environment and Climate Change Management Hon. Halima Daudi, MP. and Mr. Asbjorn Edihammer, the Norwergian Ambassador to Malawi.

The radio station covers the Lake Chilwa basin and its surrounding areas, reaching Zomba, Machinga, Phalombe, Chiradzulu, Mangochi, and Mulanje districts.

The main objective of the station is to provide information on climate change adaptation, natural resource management, health, education, and other developmental programmes. This is in line with our vision, we provide capacity building for other community radios and train media students from Chancellor College and other colleges in broadcasting skills. In this regard, the station specifically provides opportunities for students from Chancellor College Department of Language and Communication Studies (LACS) to train in radio journalism. We also have a total of 11 radio listening clubs scattered across Zomba, Phalombe and Machinga Districts. These radio listening clubs were trained in programme production and content gathering and we continue to actively support their activities.

Over the years, Chanco Community Radio has partnered with different government agencies and non-governmental organisations in the implementation of different projects within the Lake Chilwa Basin. These organisations include Leadership for Environment and Development - South East Africa (LEAD-SEA), WorldFish, and Forestry Institute of Malawi (FRIM) through the Lake Chilwa Climate Change Adaptation Programme. Our success story cannot be complete without the mention of organisations with which we have worked in different capacities such as National AIDS Commission (NAC), USAID through SSDI, UNICEF, Save the Children, FMB, NBS Bank, Farm Radio Trust (FRT), Pakachere Institue of Health and Development Communication, JHPIEGO, and PACT Malawi, among many others.