
19/07/2025
Yemwe akufuna kuzayimira ngati phungu wakunyumba yamalamulo woyima payekha mdera la Zomba Changalume a Golden Galeza apempha achinyamata omwe analembetsa mukawundula kuti akaponye voti mwaunyinji pachisankho chikubwerachi.
Iwo ayankhula izi pa mkumano omwe anayitana achinyamata ndikuwagawira mfundo zomwe azachite akazapambana pa chisankho.
Iwo anati achinyamata akuyenera kukhala patsogolo pokavota kuti zinthu zisinthe ponena kuti chiwelengero chochuluka mdziko muno ndi cha achinyamata poyelekeza ndi amayi komanso abambo.
Mmawu ake, woyimira achinyamata kudelari a Idrissa Malenga anati achinyamata ambiri amangogwiritsidwa ntchito ndi andale koma akasankhidwa saganizira mavuto awo.
Iye anati pali ntchito zambri zomwe achinyamata angagwire zotukula dera koma zimangosowekera upangiri wa atsogoleri amasomphenya kuti ntchitozi zipite patsogolo.
Wolemba Peter Davieson