07/28/2022                                                                            
                                    
                                                                            
                                            ALINAFE 
                                      Part 4 .....  
Ngakhale kunja kunali kukuda Alinafe sizimamukhudza chomwe amangosamala iye ndiza jimmy 
Koma mosakhalitsa anasiyana,, naye Nafe anayenda changu kukafika ndipo atafika kwawo kunali kuyankhulidwa.........
Mai: nthawi yobwera munthu pakhomo ino ? Pakhomo pano pakukwana eti ingosamuka upeze banja lako uzibwera nthawi yomwe ufune 
Nafe: Pepan kungoo......
Mai: Pepan ndekuti chani ?? Nde umati ataphike ndi ndani nthaw zino kapena umafuna uzapeze akapolo ako atakuphikira eti,,,,, Kuli ma Poto  ukukuziwa ngati njala ikupweteka ukaphika..........
Atayankhula chonchi Alinafe sanayankhulenso kalikonse mmalo mwake anakangolowa Kuchipinda kwake Ndikumakagona, mosakhalitsa Martha naye analowa Komko...
Martha: Nafe Ukugona sudya ?? 
Nafe: Eya ndili Okhuta Dear Osadandaula Ndadya ku School ku nzanga anabweretsa zakudya 
Martha: Ai ukundinamiza ukufuna kungondinyengelera iwe dzuka chonde ukaphike ndikakudikira 
Nafe: mmh Zoona tu koma ndili okhuta kwambiri or ndikaphike sindikwanitsa kudya 
Kukana kwa Nafe kuphika izi zinamukwiyitsa martha ndipo ananyanyala kuyamba kulira zomwe zinapangitsa Nafe kunva chisoni koma zinali zomuvutabe kuti angakaphike maka mau opweteka omwe anayankhulidwawo ..... Mwachoncho anagona ............
Miyezi inali ikupita masikunso mkumatha ndipo mthawi yoti A form 4 alembe mayeso inakwana ndipo ama Class enawa anapatsidwa Holiday...
Kwa nthawi yomwe Nafe anali pakhomo nthawi ya Holiday anangosandukano ngati kapolo kuchita kukhumba atangotsegulira kuti nthawi ina azikhala ali ku School komaso akalingalira kumusowa Jimmy zimamupweteka kwambiri... Kenako tsiku lina ali khale kuchipinda kwake anaitanidwa
Mai: Alinafe !!!! 
Nafe: Weeee Mah.......
Mai: Ukutan ?!
Nafe: ndimalemba zina zake zaku School
Mai: Okay komano School ikuoneka kuti ivuta maka Fees siipezekanso nde term inoyi ikatha basi School yonso yathera pompo
Nafe: Ahm ahm (Mosakhalitsa Nafe anayamba kugwetsa misonzi kusowa choti angayankhe kenako anakalowanso nyumba)
Izitu zinalo zifukwa zokwanira kumukhazika Nafe Okhumudwa ndi chakudya chomwe samachinva kukoma,, Umoyo wa Nafe unasinthiratu ndipo maganizo anamuchulukiliratu kwanthawi yochepa anachita Kuonda Nafe ......
Mayeso anamalizidwa ndipo achina Nafe anabwelera Ku school ndipo tsiku li atangofika anali ndi chikhulupiliro kuti Jimmy ali komko kumudikira iyeyu nde naye Nafe sanachedwe koma kuyamba kumusaka Jimmy.... Mosakhalitsa anangoti Maso Phaaaaaa,, apa tu aliyense kunali kuyenda mwachangu ndikukumbatirana kwaka nthawi uku akauuzana monong'ona kuti ndakusowa.........
Jimmy: Nafe ndakusowa koma 
Nafe: ineso kwambiri ndipo tsiku ndi tsiku ndimaganizira iweyo mamunanga 
Jimmy: ukumaganiza kwambiri koma eti Nafe
Nafe: iiiih Jimmy sungazinvetse koma ngakhale ili nkhani yaitali komanso ngakhale ndinayamba kukubisira kale kale osamakuuza leroli ndikuuza chili chonse 
"Nafe anayambapo kufotokoza chili chonse mene amakhalira kwawo komanso zokhudza kusiya kwake kwa School Chifukwa cha Fees" ...... Mene amamaliza izi kuyankhula Naye Jimmy nkhope yake inaoneka yokhumudwa ndipo poyankhula panachita kumusowa poyambira..
Jimmy: Okay nafe ndanva Ndizosakhala bwino koma ndili ndi Plan ineyo ndipeza njira ndipo School yako itheka wanva Osadandaula ndimakukonda 
Nafe: zikomo kwambiri Jimmy koma nde upanga motani ?
Jimmy: koma nafe Nthawi ikutha tu umayenera ukalowe Class
Nafe: Inayi ndikufuna kungokhala ndiweyo lero sindkulowa Class ine....... Ali mkati mocheza ananva Belu kulira ndipo uku kunali kuitana Ophunzira kuti akakhale pa Assembly zomwe zinasonyeza kuti pali uthenga wapadera mosakhalitsa ophunzira onse anakhamukira komweko ndipo aliyense anali tcheru kuti anva Chani...
Mr kasiya (Mphunzitsi): Uthenga Wachisoni Mmodzi mwa aziphunzitsife waitisiya nde ndi dongosolo lomwe likhale pa mwambo onse kuti uthe ndiwautaliko nde munkhala ndi week ya Holiday muzabwerenso Lolemba linalo zikomo.. Anayankhula Choncho Mphuzitsiyo akuoneka okhumudwa ... Atabalalika Ophunzira aja aliyense kumaona Kolowera naye Jimmy ndi Nafe nawo analowera kwawo  komwe anakakhala ndkumachezetsana atagula zokudya zao ukukumadyetsananso zachikondi zija ............. 
Kunena zoona Nafe amanva kukoma akakhala ndi Jimmy pafupi amayiwaladi Zambiri ....
Nafe: jimmy ndaganiza Mofatsa Kunyumba Za Holiday yi sindikanena ubwino wakenso sangaziwe kali konse nde Daily ndizinyamuka ngati ndikubwera Ku School tizikumana Daily ndikufuna ndizingokhala ndiweyo 
Jimmy: Oooh yah ndazikonda nde malo mwake mawalo tikakumana ndikutenga ukaziwe kunyumba
Nafe: kwanu ai sindizizamasuka  
Jimmy: Ai anthu onse kumakhala kulibe tizakakhala awiri wiri Momasukanso 
Nafe: chabwino ndizatero
Jimmy: Eya ndipo osangoti mawa Lokhaliyi koma week yonsei akuapatsani Holiday yi uzingobwera straight kunyumba tizakhala ngati banja basi......."""hahahahaha !!, onse anaseka""..........
Awiriwa anacheza mpaka chakumadzulo kenako anasiyana onse ndikumapita kwawo.... Usiku watsikuli Nafe unamutalikira kuona kuchedwa kuti Kuche koma mopilira momo kunachadi ndipo Nafe anakonzeka bwino lomwe ngati akupita ku School koma akuti azinyamuka......
Mai: Ukupita kuti 
Nafe: Ku School
Mai: mesa Lucy ndinamutumira kuti akuuze kuti lero usapite ku School ndikufuna ndikutume
Nafe: Sanandiuze tu ine ndipo....
Mai: Chokaaa ukupangira Dala iwe koma ndakuuza apa ndikusamba Kaye 
"Nafe anachita kuziona ngati dziko lamuthera atabalalikiratu ndizosemphana ndizomwe amayembekezera kuzifunsa kuti kuona kuchedwa konse kuja amaonera kuchedwera zimenezi"
Mtima unamuwawa kwambiri ndipo anakanika kupilira mpaka anaganiza zongothawa basi ndipo mpaka anachoka mwakachetechetedi Mai osaziwa anangodabwa ziii munthu kulibe .....................
Nafe Anakumana Ndi Jimmy monga mene anagwiliziranirana kenako anatengana ndikumapita kwawo kwa Jimmy.... 
Jimmy: lero nyumba ndiyathu timasuke ngati Banja lero ndidye zophika akazanga
(Hahahhaahhahahahaha) onse anasekelera mosakhalitsa jimmy anamuza nafe kuti athandizane kuphika zakudya,,,,, atamaliza anakhala ndithu onse ndikudya limodzi monga Banja........ Nkhani zawo zinali pakamwa uku akumenyana mwachikondi mpaka kumagwirananso mwakamodzi onse anakhala chete ngati kwagwa chivomerezi ndipo panthawi mkuti aliyense akuyang'ana mmaso mwanzake ndipo mosachedwa zodyana milomo zinayambika Nafe anakumbukira tsiku lake loyamba lija anapangaso ndi jimmy lija anazinva kukoma kwambiri ndipo anakanika kuti amusiye Jimmy ndipo samkaziwa kuti kwinako zimapitilira bwanji komano anafuna atazilawa mene zimakhalira mosakhalutsa Nafe anayamba kumuchotsa zovala Jimmy naye Jimmy sanachedwe koma kuchotsa Zovala Nafe ..........ziiiiiiii ๐๐๐ game inaseweredwa mbambande Mpaka Nafe anachita kuzinva ngati ali dziko lina...
Nafe: Jimmy sindkwanitsa ine ineyo jimmy ndineyo wako Jimmy chita nane chonde
"hahahahha Nafe anayamba kuyankhula ngati wapenga nkhani zovuta kulumikizika kuti akufuna kunena chani"..........
Linali tsiku lokoma kwa Nafe ndipo amkachita kuona kuluza kuti asiyane ndi jimmy koma poti kunja nthawi imapita ndipo anayenera kubwelera mmbuyo kenako jimmy anamuperekeza Nafe ndikumupatsa ndalama yoti azigwiritsa ntchito..........
Nafe atafika kwawo nanji machokedwe anali ochita kuthawa ,,,, hahahahahaha zinaliko ukuuuu tiyeni tione mu Part yotsatirayo ..
๐Like
โComment
๐Share 
๐ป Hes ๐